আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
238 : 2

حَٰفِظُواْ عَلَى ٱلصَّلَوَٰتِ وَٱلصَّلَوٰةِ ٱلۡوُسۡطَىٰ وَقُومُواْ لِلَّهِ قَٰنِتِينَ

Sungani mokwanira Swala makamaka Swala yapakatikati; ndipo imilirani modzichepetsa kwa Allah.[41] info

[41] M’ndime iyi akulimbikitsa kuti Swala zonse anthu azipemphere muunyinji wawo osati munthu payekhapayekha makamaka Swala yapakatikati. Ena mwa maulama adati Swala yapakatikati ndi Swala ya Dhuhr. Imapempheredwa pakatikati pamasana, dzuwa litatentha kwambiri monga momwe zilili m’maiko a Arabu. Pa Swala ya Dhuhr anthu amavutika kwambiri kukapemphera m’misikiti chifukwa chakutentha kwa dzuwa. Choncho apa akuwalimbikitsa kuti azikapemphera m’misikiti ngakhale kuli kotentha. Pomwe ena akuti Swala yapakatikati ndi Swala ya Fajiri (Subuh) imene imapempheredwa pakatikati panthawi. Simasana ndiponso siusiku. Apa mpanthawi pomwe tulo timakhala tamphamvu. Tero akuwalimbikitsa anthu kusiya tuloto nkupita ku misikiti nkukapemphera Swala ya (jama) yapagulu. Ndipo akutilimbikitsanso kuti tizipemphera mofatsira ndi modzichepetsa. Ndikuti tikamapemphera tizidziwa kuti taimilira pamaso pa Allah. Komanso ma hadith ena atchula zakuti Swala yapakatikati ndi Swala ya Asr.

التفاسير:

external-link copy
239 : 2

فَإِنۡ خِفۡتُمۡ فَرِجَالًا أَوۡ رُكۡبَانٗاۖ فَإِذَآ أَمِنتُمۡ فَٱذۡكُرُواْ ٱللَّهَ كَمَا عَلَّمَكُم مَّا لَمۡ تَكُونُواْ تَعۡلَمُونَ

Ndipo ngati muli ndi mantha (kupemphera mwalamulo pamene mukumenyana ndi adani anu), pempherani uku mukuyenda, kapena mutakwera chokwera. Ndipo mukakhala pachitetezo mkumbukireni Allah (pempherani) monga momwe wakuphunzitsirani zomwe simudali kuzidziwa. info
التفاسير:

external-link copy
240 : 2

وَٱلَّذِينَ يُتَوَفَّوۡنَ مِنكُمۡ وَيَذَرُونَ أَزۡوَٰجٗا وَصِيَّةٗ لِّأَزۡوَٰجِهِم مَّتَٰعًا إِلَى ٱلۡحَوۡلِ غَيۡرَ إِخۡرَاجٖۚ فَإِنۡ خَرَجۡنَ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ فِي مَا فَعَلۡنَ فِيٓ أَنفُسِهِنَّ مِن مَّعۡرُوفٖۗ وَٱللَّهُ عَزِيزٌ حَكِيمٞ

Ndipo mwa inu amene amwalira nasiya akazi awo, alangize (amlowam’malo awo, monga makolo ndi achibale) za akazi awo kuti awapatse zodyera m’nyengo ya chaka chimodzi popanda kutulutsidwa (m’nyumba zomwe ankakhala ndi amuna awo). Koma ngati akaziwo atuluka (okha), palibe kulakwa pa inu pa zimene adzichitira okha zomwe nzogwirizana ndi chilamulo cha Shariya. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
241 : 2

وَلِلۡمُطَلَّقَٰتِ مَتَٰعُۢ بِٱلۡمَعۡرُوفِۖ حَقًّا عَلَى ٱلۡمُتَّقِينَ

Ndipo akazi osiidwa ukwati, apatsidwe chilekaniro chowasangalatsa m’chilamulo cha Shariya. Ili ndi lamulo kwa amene akuopa Allah.[42] info

[42] Pamene mwamuna akumusiya mkazi ukwati pafunika kuti ampatse chinthu china kuwonjezera pa chiwongo. Koma Asilamu ambiri kudera la kuno kum’mawa kwa Afrika m’malo mompatsa chinthu mkazi pomusiya amaitanitsa chinthu kwamkazi kuti awapatse kapena kumlanda katundu kumene.
Machitidwe otere ngoipitsitsa, sali ogwirizana ndi malamulo a Chisilamu.

التفاسير:

external-link copy
242 : 2

كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمۡ ءَايَٰتِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ

Umu ndi momwe Allah akukulongosolerani ma Ayah ake (ndime zake) kuti inu mukhale ndi nzeru. info
التفاسير:

external-link copy
243 : 2

۞ أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ خَرَجُواْ مِن دِيَٰرِهِمۡ وَهُمۡ أُلُوفٌ حَذَرَ ٱلۡمَوۡتِ فَقَالَ لَهُمُ ٱللَّهُ مُوتُواْ ثُمَّ أَحۡيَٰهُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَشۡكُرُونَ

Kodi sudamve (nkhani za) amene adatuluka m’nyumba zawo ali zikwizikwi kuopa imfa? Ndipo Allah adawauza: “Mwalirani,” (ndipo adamwalira chabe popanda chifukwa chilichonse). Kenako Adawaukitsa (kuti adziwe kuti imfa njosathawika). Ndithudi, Allah Ndimwini kuchita zabwino pa anthu, koma anthu ambiri sathokoza.[43] info

[43] Ibun Abbas adati anthuwo adali zikwi zinayi. Adatuluka m’nyumba zawo kuthawa mliri wanthomba, nati pakati pawo: “Tipite kudziko lina komwe kulibe mliri wanthomba.” Choncho adayenda mpaka kufika pamalo pena; ndipo Allah adati kwa iwo: “Mwalirani,” ndipo onse anamwaliradi nthawi yomweyo. Ndipo mmodzi wa aneneri adawadutsa iwo ali akufa, nampempha Allah kuti awawukitse kuti azimgwadira. Choncho adawaukitsa. Nkhaniyi tikuphunziramo zoti imfa siithawika.

التفاسير:

external-link copy
244 : 2

وَقَٰتِلُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٞ

Ndipo menyani nkhondo panjira ya Allah, ndipo dziwani kuti Allah Ngwakumva, Ngodziwa chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
245 : 2

مَّن ذَا ٱلَّذِي يُقۡرِضُ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنٗا فَيُضَٰعِفَهُۥ لَهُۥٓ أَضۡعَافٗا كَثِيرَةٗۚ وَٱللَّهُ يَقۡبِضُ وَيَبۡصُۜطُ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ

Kodi ndani angamkongoze Allah ngongole yabwino (yochokera m’chuma chake powapatsa amphawi ndi kupereka pa njira ya Allah) kuti amuonjezere zoonjezera zambiri? Ndipo Allah ndi yemwe amafumbata ndi kutambasula, ndipo kwa Iye nkumene mudzabwezedwa.[44] info

[44] Apa anthu akuwalimbikitsa kuti azipereka chuma chawo pa njira zabwino ndipo Allah adzawalipira mphoto yambiri. Asachite umbombo kupereka chuma chawo m’njira zabwino pakuti sadaka siichepetsa chuma koma kuchichulukitsa.

التفاسير: