আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
146 : 2

ٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ يَعۡرِفُونَهُۥ كَمَا يَعۡرِفُونَ أَبۡنَآءَهُمۡۖ وَإِنَّ فَرِيقٗا مِّنۡهُمۡ لَيَكۡتُمُونَ ٱلۡحَقَّ وَهُمۡ يَعۡلَمُونَ

Aja amene tidawapatsa buku akumuzindikira (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) monga momwe amawazindikilira ana awo. Koma ena mwa iwo akubisa choonadi uku akudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
147 : 2

ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُمۡتَرِينَ

(Kuyang’ana ku Al-Kaaba popemphera Swala ndicho) choonadi chomwe chachokera kwa Mbuye wako, choncho usakhale mmodzi mwa openekera. info
التفاسير:

external-link copy
148 : 2

وَلِكُلّٖ وِجۡهَةٌ هُوَ مُوَلِّيهَاۖ فَٱسۡتَبِقُواْ ٱلۡخَيۡرَٰتِۚ أَيۡنَ مَا تَكُونُواْ يَأۡتِ بِكُمُ ٱللَّهُ جَمِيعًاۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ

Ndipo (mpingo) uliwonse udali ndi chibula chimene udali kuchilunjika. Choncho pikisanani pochita zabwino. Paliponse pamene mungakhale Allah adzakubweretsani nonsenu pamodzi (pa tsiku la chimaliziro). Ndithudi, Allah Ngokhoza chinthu chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
149 : 2

وَمِنۡ حَيۡثُ خَرَجۡتَ فَوَلِّ وَجۡهَكَ شَطۡرَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِۖ وَإِنَّهُۥ لَلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَۗ وَمَا ٱللَّهُ بِغَٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ

Ndipo paliponse pomwe wapita tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika (panthawi yopemphera). Chimenecho nchoonadi chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita. info
التفاسير:

external-link copy
150 : 2

وَمِنۡ حَيۡثُ خَرَجۡتَ فَوَلِّ وَجۡهَكَ شَطۡرَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِۚ وَحَيۡثُ مَا كُنتُمۡ فَوَلُّواْ وُجُوهَكُمۡ شَطۡرَهُۥ لِئَلَّا يَكُونَ لِلنَّاسِ عَلَيۡكُمۡ حُجَّةٌ إِلَّا ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡهُمۡ فَلَا تَخۡشَوۡهُمۡ وَٱخۡشَوۡنِي وَلِأُتِمَّ نِعۡمَتِي عَلَيۡكُمۡ وَلَعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ

Paliponse pamene wapita (iwe Mtumiki {s.a.w}) tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika. Ndipo paliponse pamene (inu Asilamu) muli tembenuzirani nkhope zanu kumbali yake (ya Msikitio) kuti anthu asakhale ndi mtsutso pa inu, kupatula amene adzichitira zoipa mwa iwo. Tero musawaope, koma opani Ine, ndipo ndikwaniritsa chisomo Changa pa inu kuti muongoke. info
التفاسير:

external-link copy
151 : 2

كَمَآ أَرۡسَلۡنَا فِيكُمۡ رَسُولٗا مِّنكُمۡ يَتۡلُواْ عَلَيۡكُمۡ ءَايَٰتِنَا وَيُزَكِّيكُمۡ وَيُعَلِّمُكُمُ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحِكۡمَةَ وَيُعَلِّمُكُم مَّا لَمۡ تَكُونُواْ تَعۡلَمُونَ

Monganso tamtumizira Mtumiki (s.a.w) kwa inu wochokera mwa inu kuti akuwerengereni Ayah (ndime) Zathu, ndikukuyeretsani (kuuve wopembedza mafano) ndi kukuphunzitsani buku ndi nzeru, ndikukuphunzitsani zimene simunali kuzidziwa. info
التفاسير:

external-link copy
152 : 2

فَٱذۡكُرُونِيٓ أَذۡكُرۡكُمۡ وَٱشۡكُرُواْ لِي وَلَا تَكۡفُرُونِ

Choncho ndikumbukireni (pondithokoza pa mtendere umene ndakupatsaniwu). Nanenso ndikukumbukirani (pokulipirani mphoto yaikulu). Ndipo ndiyamikeni; musandikane. info
التفاسير:

external-link copy
153 : 2

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱسۡتَعِينُواْ بِٱلصَّبۡرِ وَٱلصَّلَوٰةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ مَعَ ٱلصَّٰبِرِينَ

E inu amene mwakhulupirira! Dzithandizeni (pa zinthu zanu) popirira, ndi popemphera Swala. Ndithudi, Allah ali pamodzi ndi opirira. [7] info

[7] M’ndimeyi Allah akulangiza Asilamu kuti akhale opilira pa masautso amtundu uliwonse amene akukumana nawo. Kupilira ndi chida chakuthwa chopambanitsa munthu ndi kugonjetsera masautso. Munthu wosapilira ndi zopweteka sangapambane pa zofuna zake. Allah akutilangizanso kuti tifunefune chithandizo pochulukitsa Swala chifukwa chakuti imalimbitsa mtima wa munthu pa masautso. Mtumiki (s.a.w) ankati masautso akamukhudza amachita changu kukapemphera Swala. Ndipo ankayankhula kuti: “Allah waupanga mpumulo wanga kukhala mkati mwa Swala.”

التفاسير: