[34] Mwamuna akalumbira kuti sakhala naye pamodzi mkazi wake, tero mkaziyo ayembekezere nthawi yamiyezi inayi. Ndipo ngati nthawiyi ipambana asanakhalebe naye pamodzi, apite akamsumire kwa Kadhwi (mkulu wodziwa malamulo a Chisilamu). Ndipo Kadhwiyo akakamize mwamunayo kuti akhale naye pamodzi mkazi wakeyo, apo ayi, awalekanitse ngati izo zitalephereka. Sibwino kuvutitsana pakati pa anthu makamaka pakati pa mwamuna ndi mkazi.
[35] Mkazi ngati amsudzula ukwati saloledwa kukwatiwa ndi mwamuna wina mpaka Edda yake ithe. Ndipo Edda njosiyanasiyana kwa akazi. Eddayi njotere kusiyana kwake:
1. Mkazi akasiyidwa ali ndi mimba, pamenepo ndiye kuti Edda yake imatha akangobereka. Pompo mwamuna wina akhoza kumkwatira.
2. Ngati wosiidwayo ndi mkazi yemwe sadwala matenda akumwezi
(a) chifukwa chakukalamba
(b) kapena chifukwa chakuti sanakwane zaka zoyambira kudwala kumweziko
(c) kapena chifukwa chakuti chilengedwe chake chili momwemo
(d) kapena zifukwa zina zomwe zimachititsa kuti asadwale matenda akumwezi edda yawo onsewa ndimiyezi itatu. Asakwatiwe mpaka miyezi itatu ithe kuchokera patsiku lomwe adawasudzula.
3. Ngati wosudzulidwayo ndimkazi wodwala matenda akumwezi, Edda yake imatha akamaliza “khului” zitatu. Tsono tanthauzo lakhului maulama amamasulira mosiyanasiyana. Pamazihabi a Imam Shafii tanthauzo lake ndikuyeretsedwa kutatu (twahara zitatu). Choncho kuyeretsedwa kutatuku kukatha kuyambira pomwe adamsudzula, akhoza kukwatiwa. Koma pamazihabi a Kibazi tanthauzo lake ndikudwala kumwezi katatu (hizi zitatu). Kukatha kudwala kumwezi kutatu komwe kwachitika pambuyo pamsudzulo ndiye kuti akhoza kukwatiwa. Edda ngati siinathe mkazi saloledwa kukwatiwa. Ngati atakwatiwa ali mu edda ukwatiwo suvomerezeka. Ndiye kutinso nthawi yonse yomwe mkaziyo akukhala limodzi ndi mwamunayo akuchita naye chiwerewere. Ndipo amene akubadwa mu ukwati wotere ndi ana obadwira mu chiwerewere. Akazi omwe asiidwa ukwati akuwalangiza kuti asabise mimba kuti mwanayo adzadziwike tate wake. Ngati Edda siinathe ndiponso ngati kuchuluka kwa twalaka mwamuna sadamalize, mwamunayo ali ndi ufulu wobwererana ndi mkazi ngati atafuna. Tero padzangofunika kupeza mboni ziwiri zoti zimdziwitse mkaziyo kuti mwamuna wake wabwererana naye. Mkaziyo kapenanso abale ake saloledwa kukaniza zimenezo.
[36] Apa akuletsa kumlanda kanthu mkazi kapena kumuuza kuti abweze mahari (chiwongo). Pamalo pamodzi pokha mpomwe pali povomerezeka mkazi kudziombola kwa mwamuna wake ngati mkaziyo njemwe wafuna kuti ukwatiwo uthe, ndiponso ngati palibe choipa chilichonse chomwe mwamunayo akuchita ndipo sangathe kukhala naye mwa mtendere. Pamenepa ndiye kuti mkaziyo abweze chiwongo kuti adzichotsemo muukwati woterowo.