[52] Mneneri Ibrahim adalakalaka kuti aone mmene akufa adzaukira kuti chikhulupiliro chake chiwonjezeke mphamvu. Tero Allah adamulamula kuti azinge mbalame zinayi zosiyanasiyana mitundu. Kenako azisakanize ziwalo zake. Ziwalo za mbalame ina zilowe kumbalame ina. Tsono azigawe miyulu inayi. Mulu uliwonse akauike pa phiri lakelake. Kenako aziitane mbalame zija. Ndipo aona kuti chiwalo chilichonse chikuthamangira kumbalame yake, pompo zonsezo zikhalanso mbalame zamoyo monga momwe zidalili poyamba.
[53] (Ndime 261-267) zikulimbikitsa kupereka chuma pa njira zabwino ndiponso zikuonetsa ubwino umene woperekayo amalandira kwa Allah. Komatu woperekayo kuti apeze ubwino wa Allah pafunika izi:
(a) apereke chifukwa cha Allah osati ncholinga chodzionetsera kwa anthu,
(b) choperekacho chikhale chabwino. Ngati wapereka zomwe sizabwino ndiye kuti sangapeze mphoto yaikulu,
(c) asawakumbe amene akuwapatsawo.
(d) Asawavutitse. Ndipo ngati atachita zimenezi ndiye kuti sangapeze mphoto koma kungotaya chuma pachabe. Kumbwezera mawu abwino wopempha nkopindulitsa kuposa sadaka yotonzera.
(e) Chimene akuperekacho chikhale chaHalali (chololedwa).Osati chomwe adachipeza m’njira yosavomerezeka.