[41] M’ndime iyi akulimbikitsa kuti Swala zonse anthu azipemphere muunyinji wawo osati munthu payekhapayekha makamaka Swala yapakatikati. Ena mwa maulama adati Swala yapakatikati ndi Swala ya Dhuhr. Imapempheredwa pakatikati pamasana, dzuwa litatentha kwambiri monga momwe zilili m’maiko a Arabu. Pa Swala ya Dhuhr anthu amavutika kwambiri kukapemphera m’misikiti chifukwa chakutentha kwa dzuwa. Choncho apa akuwalimbikitsa kuti azikapemphera m’misikiti ngakhale kuli kotentha. Pomwe ena akuti Swala yapakatikati ndi Swala ya Fajiri (Subuh) imene imapempheredwa pakatikati panthawi. Simasana ndiponso siusiku. Apa mpanthawi pomwe tulo timakhala tamphamvu. Tero akuwalimbikitsa anthu kusiya tuloto nkupita ku misikiti nkukapemphera Swala ya (jama) yapagulu. Ndipo akutilimbikitsanso kuti tizipemphera mofatsira ndi modzichepetsa. Ndikuti tikamapemphera tizidziwa kuti taimilira pamaso pa Allah. Komanso ma hadith ena atchula zakuti Swala yapakatikati ndi Swala ya Asr.
[42] Pamene mwamuna akumusiya mkazi ukwati pafunika kuti ampatse chinthu china kuwonjezera pa chiwongo. Koma Asilamu ambiri kudera la kuno kum’mawa kwa Afrika m’malo mompatsa chinthu mkazi pomusiya amaitanitsa chinthu kwamkazi kuti awapatse kapena kumlanda katundu kumene.
Machitidwe otere ngoipitsitsa, sali ogwirizana ndi malamulo a Chisilamu.
[43] Ibun Abbas adati anthuwo adali zikwi zinayi. Adatuluka m’nyumba zawo kuthawa mliri wanthomba, nati pakati pawo: “Tipite kudziko lina komwe kulibe mliri wanthomba.” Choncho adayenda mpaka kufika pamalo pena; ndipo Allah adati kwa iwo: “Mwalirani,” ndipo onse anamwaliradi nthawi yomweyo. Ndipo mmodzi wa aneneri adawadutsa iwo ali akufa, nampempha Allah kuti awawukitse kuti azimgwadira. Choncho adawaukitsa. Nkhaniyi tikuphunziramo zoti imfa siithawika.
[44] Apa anthu akuwalimbikitsa kuti azipereka chuma chawo pa njira zabwino ndipo Allah adzawalipira mphoto yambiri. Asachite umbombo kupereka chuma chawo m’njira zabwino pakuti sadaka siichepetsa chuma koma kuchichulukitsa.