Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

Al-lnshiqâq

external-link copy
1 : 84

إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنشَقَّتۡ

Pamene thambo lidzang’ambike (kusonyeza mapeto ake), info
التفاسير:

external-link copy
2 : 84

وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ

Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero, info
التفاسير:

external-link copy
3 : 84

وَإِذَا ٱلۡأَرۡضُ مُدَّتۡ

Ndiponso pamene nthaka idzatambasulidwe (pogumuka mapiri ake ndikuchoka zitunda zake), info
التفاسير:

external-link copy
4 : 84

وَأَلۡقَتۡ مَا فِيهَا وَتَخَلَّتۡ

Ndi kutaya zomwe zidali mkati mwake ndi kukhala yopanda kanthu,[405] info

[405] Chimodzi mwa zinthu zoopsa zomwe zidzachitika tsiku lachimaliziro ndi kugwedezeka kwa nthaka mwamphamvu zedi mpaka idzalekana ndi mapiri amene ali zichiri zake zoletsa kugwedezeka kwake. Pachifukwa ichi idzatambasuka ndipo zomwe zidali mkati mwake zidzatulukira pamtunda; nthaka idzangokhala yopanda kanthu mkati mwake.

التفاسير:

external-link copy
5 : 84

وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ

Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero. (Choncho zikadzachitika zimenezi ndiye kuti munthu adzalandira mphoto ya zochita zake).[406] info

[406] Allah pambuyo ponena zimenezi sadanene kuti chidzachitika chiyani. Alekera munthu mwini wake kuti aganizire chomwe chidzachitika zikadzapezeka zoopsa kuti aope kwambiri.

التفاسير:

external-link copy
6 : 84

يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡإِنسَٰنُ إِنَّكَ كَادِحٌ إِلَىٰ رَبِّكَ كَدۡحٗا فَمُلَٰقِيهِ

E iwe munthu! Ndithudi iwe ukubwerera kwa Mbuye wako (ndi zochita zako zabwino kapena zoipa), kubwerera kotsimikizika, ndipo iwe ukumana (ndi zotsatira za zochitachita zako). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 84

فَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ

Tsono amene adzapatsidwe kaundula wa zochita zake kudzanja la manja,[407] info

[407] Tsiku la chiweruziro munthu adzapatsidwa kaundula wake monga momwe zanenedwa mu Ayah 10 Surah Takwir, choncho ena adzapatsidwa ndi dzanja la kumanja; iwo ndiwo anthu abwino. Pomwe ena adzapatsidwa ndi dzanja la kumanzere, chakumbali yakumsana; iwowo ndiwo anthu oipa.

التفاسير:

external-link copy
8 : 84

فَسَوۡفَ يُحَاسَبُ حِسَابٗا يَسِيرٗا

Basi iye, adzawerengedwa, kuwerengedwa kopepuka,[408] info

[408] Anthu ena adzawerengedwa popanda kufunsidwa mafunso pa zimene adachita, koma adzangowauza zabwino zawo ndi zoipa zawo ndipo pambuyo pake adzawakhululukira zoipazo ndi kudzawalipira pa zabwinozo. Iwowa ndiwo anthu abwino; chimenechi ndicho chiweruzo chofewa. Ena adzaweruzidwa pofunsidwa pa chilichonse m’zimene ankachita monga kuti “Bwanji ichi udachita? Bwanji ichi sudachite”? Iwowa ndiwo anthu oipa; chiwerengero chawo chidzakhala chokhwima.

التفاسير:

external-link copy
9 : 84

وَيَنقَلِبُ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورٗا

Ndipo adzabwerera kwa anthu ake (okhulupirira) ali wokondwa. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 84

وَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ وَرَآءَ ظَهۡرِهِۦ

Koma yemwe adzapatsidwe kaundula wa zochita zake chakumanzere kudzera kumbuyo kwa msana wake (chifukwa chomunyoza), info
التفاسير:

external-link copy
11 : 84

فَسَوۡفَ يَدۡعُواْ ثُبُورٗا

Basi, iye adzaitana imfa (kuti imufikire; kuti afe apumule, koma siidzamufikira); info
التفاسير:

external-link copy
12 : 84

وَيَصۡلَىٰ سَعِيرًا

Ndipo adzalowa ku Moto woyaka. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 84

إِنَّهُۥ كَانَ فِيٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورًا

Kamba kakuti iye adali wokondwa; (kukondwa kwa machimo) pamodzi ndi anthu ake (osaganizira za mathero ake). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 84

إِنَّهُۥ ظَنَّ أَن لَّن يَحُورَ

Ndithudi, amaganiza kuti sadzabwerera (kwa Allah ndiponso sadzawerengedwa). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 84

بَلَىٰٓۚ إِنَّ رَبَّهُۥ كَانَ بِهِۦ بَصِيرٗا

Chifukwa ninji (asabwelere)? Ndithu Mbuye wake adali kumuona. (Choncho alipidwa zimene adachita). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 84

فَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلشَّفَقِ

Choncho ndikulumbilira kufiira kwa dzuwa (pamene likulowa). info
التفاسير:

external-link copy
17 : 84

وَٱلَّيۡلِ وَمَا وَسَقَ

Ndi usiku ndi zimene wasonkhanitsa,[409] info

[409] Kubalalikana masana ndi chizolowezi cha anthu ndi nyama chifukwa chofunafuna zinthu zothandiza pa moyo wawo. Tsono usiku ukabwera amasonkhana ndi kukhala pamodzi. Ndipo ili ndilo tanthauzo la: “Usiku ndi zimene wasonkhanitsa.”

التفاسير:

external-link copy
18 : 84

وَٱلۡقَمَرِ إِذَا ٱتَّسَقَ

Ndi mwezi ukakwanira dangalira (lake), info
التفاسير:

external-link copy
19 : 84

لَتَرۡكَبُنَّ طَبَقًا عَن طَبَقٖ

Ndithudi mudzachoka apa kunka apa (pa moyo uno mpakana umene uli nkudza). info
التفاسير:

external-link copy
20 : 84

فَمَا لَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ

Kodi nchiyani chikuwaletsa iwo (okanira) kukhulupirira (Allah ndi kuuka kumanda, zisonyezo zake zitaonekera poyera)? info
التفاسير:

external-link copy
21 : 84

وَإِذَا قُرِئَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقُرۡءَانُ لَا يَسۡجُدُونَۤ۩

Ndipo ikawerengedwa kwa iwo Qur’an, sagwetsa pansi nkhope zawo (modzichepetsa). info
التفاسير:

external-link copy
22 : 84

بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يُكَذِّبُونَ

Koma amene sadakhulupirire akutsutsa basi (chifukwa cha makani ndi kudzikweza). info
التفاسير:

external-link copy
23 : 84

وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا يُوعُونَ

Ndipo Allah akudziwa (bwinobwino) zimene akuzisonkhanitsa. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 84

فَبَشِّرۡهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ

Choncho, auze nkhani yachilango chopweteka. info
التفاسير:

external-link copy
25 : 84

إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ أَجۡرٌ غَيۡرُ مَمۡنُونِۭ

Kupatula awo amene akhulupirira ndikuchita ntchito zabwino, kwa iwo kuli malipiro osatha.[410] info

[410] Ayah iyi ikusonyeza kuti kukhulupilira kokha sikungampulumutse munthu ku chilango cha tsiku lachimaliziro, koma nkofunikanso kuchita ntchito zabwino; m’Qur’an paliponse pamene akutchula za chikhulupiliro akutchulanso za kuchita ntchito zabwino.

التفاسير: