[405] Chimodzi mwa zinthu zoopsa zomwe zidzachitika tsiku lachimaliziro ndi kugwedezeka kwa nthaka mwamphamvu zedi mpaka idzalekana ndi mapiri amene ali zichiri zake zoletsa kugwedezeka kwake. Pachifukwa ichi idzatambasuka ndipo zomwe zidali mkati mwake zidzatulukira pamtunda; nthaka idzangokhala yopanda kanthu mkati mwake.
[406] Allah pambuyo ponena zimenezi sadanene kuti chidzachitika chiyani. Alekera munthu mwini wake kuti aganizire chomwe chidzachitika zikadzapezeka zoopsa kuti aope kwambiri.
[407] Tsiku la chiweruziro munthu adzapatsidwa kaundula wake monga momwe zanenedwa mu Ayah 10 Surah Takwir, choncho ena adzapatsidwa ndi dzanja la kumanja; iwo ndiwo anthu abwino. Pomwe ena adzapatsidwa ndi dzanja la kumanzere, chakumbali yakumsana; iwowo ndiwo anthu oipa.
[408] Anthu ena adzawerengedwa popanda kufunsidwa mafunso pa zimene adachita, koma adzangowauza zabwino zawo ndi zoipa zawo ndipo pambuyo pake adzawakhululukira zoipazo ndi kudzawalipira pa zabwinozo. Iwowa ndiwo anthu abwino; chimenechi ndicho chiweruzo chofewa. Ena adzaweruzidwa pofunsidwa pa chilichonse m’zimene ankachita monga kuti “Bwanji ichi udachita? Bwanji ichi sudachite”? Iwowa ndiwo anthu oipa; chiwerengero chawo chidzakhala chokhwima.
[409] Kubalalikana masana ndi chizolowezi cha anthu ndi nyama chifukwa chofunafuna zinthu zothandiza pa moyo wawo. Tsono usiku ukabwera amasonkhana ndi kukhala pamodzi. Ndipo ili ndilo tanthauzo la: “Usiku ndi zimene wasonkhanitsa.”
[410] Ayah iyi ikusonyeza kuti kukhulupilira kokha sikungampulumutse munthu ku chilango cha tsiku lachimaliziro, koma nkofunikanso kuchita ntchito zabwino; m’Qur’an paliponse pamene akutchula za chikhulupiliro akutchulanso za kuchita ntchito zabwino.