Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

Số trang:close

external-link copy
17 : 8

فَلَمۡ تَقۡتُلُوهُمۡ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ قَتَلَهُمۡۚ وَمَا رَمَيۡتَ إِذۡ رَمَيۡتَ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ رَمَىٰ وَلِيُبۡلِيَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ مِنۡهُ بَلَآءً حَسَنًاۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٞ

Inu simudawaphe (ndi mphamvu zanu) koma Allah ndi Yemwe anawapha; siudawagende pamene udagenda koma Allah ndi amene anawagenda (pofikitsa mchenga m’maso mwawo, wachita zimenezi) kuti awachitire zabwino Asilamu powapatsa dalitso labwino lochokera kwa Iye. Ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[193] info

[193] Pamene nkhondo idayaka moto, Mtumiki (s.a.w) adatapa mchenga naufumbata m’manja mwake naupemphelera. Kenako adaumwaza kumbali ya adani. Ndipo mchengawo udalowa m’maso mwa aliyense wa adaniwo. Pa nkhondoyi anthu osakhulupilira Allah adali ambiri kuposa Asilamu. Koma ngakhale zidali choncho, Asilamu adagonjetsa adaniwo kwathunthu. Ambiri adaphedwa, ndipo ambirinso adagwidwa monga akaidi.

التفاسير:

external-link copy
18 : 8

ذَٰلِكُمۡ وَأَنَّ ٱللَّهَ مُوهِنُ كَيۡدِ ٱلۡكَٰفِرِينَ

Izi akuchitirani (pakalipano), ndithudi Allah afooketsa ndale za osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 8

إِن تَسۡتَفۡتِحُواْ فَقَدۡ جَآءَكُمُ ٱلۡفَتۡحُۖ وَإِن تَنتَهُواْ فَهُوَ خَيۡرٞ لَّكُمۡۖ وَإِن تَعُودُواْ نَعُدۡ وَلَن تُغۡنِيَ عَنكُمۡ فِئَتُكُمۡ شَيۡـٔٗا وَلَوۡ كَثُرَتۡ وَأَنَّ ٱللَّهَ مَعَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ngati mwakhala mukufuna chiweruzo (pogwilira nsalu yovindikira Ka’aba kuti mupambane pa nkhondo), chiweruzo chakudzerani (chokomera Asilamu). Ndipo ngati musiya (kuwazunza okhulupirira kapena kusiya kunyoza Allah) chikhala chinthu chabwino kwa inu. Koma ngati mubwereza (kuwaputa) nafenso tidzabwereza (kukulangani). Gulu lanu lankhondo silikuthandizani kanthu ngakhale lichuluke chotani. Ndipo Allah ali pamodzi ndi okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 8

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَلَا تَوَلَّوۡاْ عَنۡهُ وَأَنتُمۡ تَسۡمَعُونَ

E inu amene mwakhulupirira! Mverani Allah ndi Mtumiki Wake, ndipo musamtembenukire kumbali pamene inu mukumva.[194] info

[194] (Ndime 20-23). Ndime izi zikufotokoza kuipa kwa yemwe wamvera ulaliki ndi malangizo abwino koma naunyoza, osaugwiritsa ntchito. Ndithudi, anthu otere ndi anthu oipitsitsa. Koma chofunika nchakuti tikamva mawu a Allah tigwiritse ntchito pa moyo wathu onse.

التفاسير:

external-link copy
21 : 8

وَلَا تَكُونُواْ كَٱلَّذِينَ قَالُواْ سَمِعۡنَا وَهُمۡ لَا يَسۡمَعُونَ

Ndipo musakhale monga aja achinyengo omwe akunena: “Tamva (choonadi ndipo tachisunga),” pomwe iwo sakumva (kumva kochigonjera). info
التفاسير:

external-link copy
22 : 8

۞ إِنَّ شَرَّ ٱلدَّوَآبِّ عِندَ ٱللَّهِ ٱلصُّمُّ ٱلۡبُكۡمُ ٱلَّذِينَ لَا يَعۡقِلُونَ

Ndithu nyama zoipitsitsa pamaso pa Allah ndi agonthi, abubu amene alibe nzeru, (omwe ndi aphatikizi ndi anthu achinyengo). info
التفاسير:

external-link copy
23 : 8

وَلَوۡ عَلِمَ ٱللَّهُ فِيهِمۡ خَيۡرٗا لَّأَسۡمَعَهُمۡۖ وَلَوۡ أَسۡمَعَهُمۡ لَتَوَلَّواْ وَّهُم مُّعۡرِضُونَ

Ndipo Allah akadadziwa mwa iwo (ndi kudziwa kwake kopanda chiyambi); kuti muli ubwino (pakuwamveretsa Qur’an ndi kuwazindikiritsa) akadawamveretsa. (Koma chikhalidwe chawo chili cha mtundu umenewo) ndipo ngakhale akadawamveretsa (Qur’an ndikuwazindikiritsa) akadatembenuka m’mbuyo uku akunyoza (chifukwa cha kugonjera zilakolako zawo). info
التفاسير:

external-link copy
24 : 8

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱسۡتَجِيبُواْ لِلَّهِ وَلِلرَّسُولِ إِذَا دَعَاكُمۡ لِمَا يُحۡيِيكُمۡۖ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ يَحُولُ بَيۡنَ ٱلۡمَرۡءِ وَقَلۡبِهِۦ وَأَنَّهُۥٓ إِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ

E inu amene mwakhulupirira muvomereni Allah (pa zimene akukulamulani) ndiponso muvomereni Mtumiki Wake pamene akukuitanirani ku chimene chingakupatseni moyo (wabwino wa pa dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro). Ndipo dziwani kuti Allah amatchinga pakati pa munthu ndi mtima wake (amautembenula mmene akufunira). Ndipo dziwani kuti kwa Iye mudzasonkhanitsidwa.[195] info

[195] Mu Ayah iyi akutiuza kuti chimene Mtumiki akutiitanira nchabwino kwa anthu onse, kuyambira pa dziko lapansi mpaka pa tsiku lachimaliziro. Ndiponso tikuuzidwa kuti Allah Ngokhoza chilichonse. Akhoza kuchita chilichonse pa akapolo Ake palibe chimene chingalephereke. Koma ngakhale zili tero, Allah akuzimvera chisoni zolengedwa Zake.

التفاسير:

external-link copy
25 : 8

وَٱتَّقُواْ فِتۡنَةٗ لَّا تُصِيبَنَّ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنكُمۡ خَآصَّةٗۖ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ شَدِيدُ ٱلۡعِقَابِ

Ndipo muope mazunzo (a Allah a pano pa dziko lapansi) omwe sangagwere okhawo amene adzichitira zoipa mwa inu (koma adzawagweranso amene akusiya kuletsa zoipa) ndipo dziwani kuti Allah Ngolanga kwambiri.[196] info

[196] Mu Ayah iyi anthu olungama akuwauza kuti asalekelere anthu oipa pamene akuchita zoipa zawo popanda kuwaletsa, chifukwa chakuti chilango chapadziko lapansi chikadza chimagwera oipa ndi abwino omwe, ngakhale kuti abwinowo adzapeza zabwino pa tsiku lachimaliziro. Koma zilango zapadziko lapansi zimakhala za onse. Nchimodzimodzinso ndi madalitso, akadza amakhudza anthu onse. Choncho, nkofunika kwa anthu olungama kuletsa anthu osalungama kuchita zoipa, ndi kuwalangiza kuchita zabwino.

التفاسير: