[193] Pamene nkhondo idayaka moto, Mtumiki (s.a.w) adatapa mchenga naufumbata m’manja mwake naupemphelera. Kenako adaumwaza kumbali ya adani. Ndipo mchengawo udalowa m’maso mwa aliyense wa adaniwo. Pa nkhondoyi anthu osakhulupilira Allah adali ambiri kuposa Asilamu. Koma ngakhale zidali choncho, Asilamu adagonjetsa adaniwo kwathunthu. Ambiri adaphedwa, ndipo ambirinso adagwidwa monga akaidi.
[194] (Ndime 20-23). Ndime izi zikufotokoza kuipa kwa yemwe wamvera ulaliki ndi malangizo abwino koma naunyoza, osaugwiritsa ntchito. Ndithudi, anthu otere ndi anthu oipitsitsa. Koma chofunika nchakuti tikamva mawu a Allah tigwiritse ntchito pa moyo wathu onse.
[195] Mu Ayah iyi akutiuza kuti chimene Mtumiki akutiitanira nchabwino kwa anthu onse, kuyambira pa dziko lapansi mpaka pa tsiku lachimaliziro. Ndiponso tikuuzidwa kuti Allah Ngokhoza chilichonse. Akhoza kuchita chilichonse pa akapolo Ake palibe chimene chingalephereke. Koma ngakhale zili tero, Allah akuzimvera chisoni zolengedwa Zake.
[196] Mu Ayah iyi anthu olungama akuwauza kuti asalekelere anthu oipa pamene akuchita zoipa zawo popanda kuwaletsa, chifukwa chakuti chilango chapadziko lapansi chikadza chimagwera oipa ndi abwino omwe, ngakhale kuti abwinowo adzapeza zabwino pa tsiku lachimaliziro. Koma zilango zapadziko lapansi zimakhala za onse. Nchimodzimodzinso ndi madalitso, akadza amakhudza anthu onse. Choncho, nkofunika kwa anthu olungama kuletsa anthu osalungama kuchita zoipa, ndi kuwalangiza kuchita zabwino.