Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

external-link copy
131 : 6

ذَٰلِكَ أَن لَّمۡ يَكُن رَّبُّكَ مُهۡلِكَ ٱلۡقُرَىٰ بِظُلۡمٖ وَأَهۡلُهَا غَٰفِلُونَ

Zimenezi nchifukwa choti Mbuye wako sali woononga midzi mwachinyengo pomwe eni ake ali oiwala. (Koma ankawatumizira aneneri kuti awachenjeze ndi kuwakumbutsa).[172] info

[172] Allah sapereka chilango kwa anthu asanawatumizire Mtumiki. Ndiponso sangawalange pa zinthu zomwe nzosatheka kuzizindikira, pokhapokha Mtumiki atawaphunzitsa, monga kupemphera Swala, kusala m’mwezi wa Ramadan. Koma angawalange pazomwe iwo angathe kuzizindikira kuti nzoipa; monga munthu kumchenjelera mnzake ndi zina zotero.

التفاسير: