Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

Số trang:close

external-link copy
275 : 2

ٱلَّذِينَ يَأۡكُلُونَ ٱلرِّبَوٰاْ لَا يَقُومُونَ إِلَّا كَمَا يَقُومُ ٱلَّذِي يَتَخَبَّطُهُ ٱلشَّيۡطَٰنُ مِنَ ٱلۡمَسِّۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ قَالُوٓاْ إِنَّمَا ٱلۡبَيۡعُ مِثۡلُ ٱلرِّبَوٰاْۗ وَأَحَلَّ ٱللَّهُ ٱلۡبَيۡعَ وَحَرَّمَ ٱلرِّبَوٰاْۚ فَمَن جَآءَهُۥ مَوۡعِظَةٞ مِّن رَّبِّهِۦ فَٱنتَهَىٰ فَلَهُۥ مَا سَلَفَ وَأَمۡرُهُۥٓ إِلَى ٱللَّهِۖ وَمَنۡ عَادَ فَأُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Amene akudya riba (chuma cha katapira) sadzauka (m’manda) koma monga momwe amaimira munthu okhudzidwa ndi ziwanda, mwamisala. (Ndipo) izi nchifukwa chakuti amanena: “Malonda ngolingana ndi katapira,” pomwe Allah waloleza malonda ndipo waletsa katapira. Ndipo amene wamufika ulaliki wochokera kwa Mbuye wake (woletsa katapira) nasiya, choncho chomwe chidapita nchake. Ndipo chiweruzo chake chili kwa Allah (akaona chochita naye). Koma amene abwerera (kuchita malonda a katapira), amenewo ndiwo anthu a ku Moto, mmenemo adzakhalamo nthawi yaitali.[56] info

[56] Ndime iyi yikuletsa kukongoza m’njira yakatapira. Allah akumuopseza mwamphamvu munthu wodya riba. Akumuuza kuti adziwe kuti ali pankhondo yolimbana ndi Allah. Allah akukalipa zedi kwa anthu ochita malonda akatapira. Tero pewani kuchita malonda akatapira.. Kodi inu muli ndi nyonga zomenyerana ndi Allah?

التفاسير:

external-link copy
276 : 2

يَمۡحَقُ ٱللَّهُ ٱلرِّبَوٰاْ وَيُرۡبِي ٱلصَّدَقَٰتِۗ وَٱللَّهُ لَا يُحِبُّ كُلَّ كَفَّارٍ أَثِيمٍ

Allah amachotsa madalitso pa (chuma cha) katapira ndipo amaika madalitso pa chaulere. Ndipo Allah sakonda aliyense wosakhulupirira, wamachimo ambiri. info
التفاسير:

external-link copy
277 : 2

إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتَوُاْ ٱلزَّكَوٰةَ لَهُمۡ أَجۡرُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ وَلَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ

Ndithudi, amene akhulupirira, nachita zabwino, napemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka (Zakaat), iwo akapeza malipiro awo kwa Mbuye wawo. Ndipo pa iwo sipadzakhala mantha ndiponso sadzadandaula. info
التفاسير:

external-link copy
278 : 2

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَذَرُواْ مَا بَقِيَ مِنَ ٱلرِّبَوٰٓاْ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ

E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah, ndipo siyani zimene zatsalira m’katapira, ngati inu mulidi okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
279 : 2

فَإِن لَّمۡ تَفۡعَلُواْ فَأۡذَنُواْ بِحَرۡبٖ مِّنَ ٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦۖ وَإِن تُبۡتُمۡ فَلَكُمۡ رُءُوسُ أَمۡوَٰلِكُمۡ لَا تَظۡلِمُونَ وَلَا تُظۡلَمُونَ

Ngati simuchita (zimenezo), dziwani kuti mukulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake. Ndipo ngati mulapa, maziko a chuma chanu ndi anu. Musapondereze, ndiponso musaponderezedwe. info
التفاسير:

external-link copy
280 : 2

وَإِن كَانَ ذُو عُسۡرَةٖ فَنَظِرَةٌ إِلَىٰ مَيۡسَرَةٖۚ وَأَن تَصَدَّقُواْ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

Ndipo ngati wokongola ali ndi mavuto, choncho (wokongoza) amdikire mpaka apeze bwino. Koma ngati inu (okongoza mungakhululuke pakusiya kuitanitsa ngongole) muisintha kuti ikhale sadaka, ndibwino kwa inu ngati mukudziwa (zimenezo). info
التفاسير:

external-link copy
281 : 2

وَٱتَّقُواْ يَوۡمٗا تُرۡجَعُونَ فِيهِ إِلَى ٱللَّهِۖ ثُمَّ تُوَفَّىٰ كُلُّ نَفۡسٖ مَّا كَسَبَتۡ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ

Ndipo liopeni tsiku lomwe inu mudzabwezedwa kwa Allah. Ndipo kenako munthu aliyense adzalipidwa mokwanira pa zonse zimene adachita (ndi manja ake), ndipo iwo sadzaponderezedwa. info
التفاسير: