Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

Al-Baqarah

external-link copy
1 : 2

الٓمٓ

Alif-Lâm-Mîm.[1] info

[1] Sura iyi yayamba ndi malembo a Alifabeti, monga Alif, Laam, Miim. kusonyeza kuti Qur’an yalembedwa ndi malembo amenewa omwe anthu amawagwiritsa ntchito m’zoyankhula ndi m’zolembalemba zawo. Uku ndikuwauza osakhulupilira kuti abweretse buku lawo lolembedwa ndi malembo omwe akuwadziwawo pamene iwo amanena kuti Qur’an adangoipeka yekha Muhammadi (s.a.w) siidavumbulutsidwe ndi Allah. Choncho Allah adawachalenja kuti alembe buku lawo lofanana ndi Qur’an, koma adalephera. Choncho, kulephera kwawo ndi umboni wosonyeza kuti Qur’an ndi buku lovumbulutsidwa ndi Allah.

التفاسير:

external-link copy
2 : 2

ذَٰلِكَ ٱلۡكِتَٰبُ لَا رَيۡبَۛ فِيهِۛ هُدٗى لِّلۡمُتَّقِينَ

Ili ndi Buku lopanda chipeneko mkati mwake, ndichiongoko cha (anthu) oopa Allah. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 2

ٱلَّذِينَ يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡغَيۡبِ وَيُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ

Omwe amakhulupirira zosaoneka ndi maso (monga Munda wamtendere, Moto, Angelo ndi zina zotere zomwe Allah ndi Mtumiki (s.a.w) adazifotokoza, amapemphera Swala moyenera, ndiponso amapereka m’zimene tawapatsa. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 2

وَٱلَّذِينَ يُؤۡمِنُونَ بِمَآ أُنزِلَ إِلَيۡكَ وَمَآ أُنزِلَ مِن قَبۡلِكَ وَبِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ يُوقِنُونَ

Ndi amene akukhulupirira zomwe zidavumbulutsidwa kwa iwe, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kale iwe usadadze, nakhulupiriranso motsimikiza kuti lilipo tsiku lachimaliziro. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 2

أُوْلَٰٓئِكَ عَلَىٰ هُدٗى مِّن رَّبِّهِمۡۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ

Iwowo (omwe ali ndi chikhalidwe chotere), ali pachiongoko chochokera kwa Mbuye wawo (Allah), ndipo iwowo ndi omwe ali opambana (pokapeza ulemelero wapamwamba ku Minda ya mtendere). info
التفاسير: