[236] Allah adafewetsa dzuwa ndi mwezi kuti zitumikire anthu Ake. Chilichonse mwa izo chikuyenda molingana ndi chikonzero cha Allah kufikira pamene lidzathera dziko lapansi. Allah ndi Yemwe akuyendetsa zinthu zonse za pa dziko ndi nzeru Zake zakuya, monga kuzipatsa moyo ndi kuzipatsa imfa ndi zina zotere. Allah akutifotokozera zonsezi kuti tikhale ndi chitsimikizo choti tidzakumana naye pambuyo pa imfa.
[237] Allah akuti chodabwitsa zedi kwa anthu osakhulupilira ndiko kunena kwawo kwakuti: “Kodi tikadzafa ndi kusanduka fumbi, tidzapatsidwanso moyo wina watsopano, zidzatheka bwanji zimenezi?” Ndithudi, kukana kwawo za kuuka kwa akufa nkododometsa pakuti amene adatha kulenga zinthu zikuluzikulu, monga thambo ndi nthaka, mitengo ndi zipatso, nyanja ndi mitsinje, ngokhoza kuwabweza pambuyo pa imfa yawo.