Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

Ar-Ra’d

external-link copy
1 : 13

الٓمٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِۗ وَٱلَّذِيٓ أُنزِلَ إِلَيۡكَ مِن رَّبِّكَ ٱلۡحَقُّ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يُؤۡمِنُونَ

Alif-Lâm-Mîm-Râ. Izi ndi Ayah (ndime) za buku ili (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika); ndipo chomwe chavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, nchoonadi; koma anthu ambiri sakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 13

ٱللَّهُ ٱلَّذِي رَفَعَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ بِغَيۡرِ عَمَدٖ تَرَوۡنَهَاۖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلّٞ يَجۡرِي لِأَجَلٖ مُّسَمّٗىۚ يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَ يُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّكُم بِلِقَآءِ رَبِّكُمۡ تُوقِنُونَ

Allah ndi Yemwe adatukula thambo popanda mizati imene mukuiona; kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wachifumu Waukulu, kukhazikika koyenera ndi Iye komwe kulibe chofanizira); ndipo adafewetsa dzuwa ndi mwezi (kwa anthu). Chilichonse mwa zimenezi chikupitilira kuyenda mpaka nyengo imene idaikidwa. Iye ndi Yemwe akuyendetsa zinthu; akulongosola Ayah (ndime) kuti mukhale ndi chitsimikizo pa zakukumana ndi Mbuye wanu.[236] info

[236] Allah adafewetsa dzuwa ndi mwezi kuti zitumikire anthu Ake. Chilichonse mwa izo chikuyenda molingana ndi chikonzero cha Allah kufikira pamene lidzathera dziko lapansi. Allah ndi Yemwe akuyendetsa zinthu zonse za pa dziko ndi nzeru Zake zakuya, monga kuzipatsa moyo ndi kuzipatsa imfa ndi zina zotere. Allah akutifotokozera zonsezi kuti tikhale ndi chitsimikizo choti tidzakumana naye pambuyo pa imfa.

التفاسير:

external-link copy
3 : 13

وَهُوَ ٱلَّذِي مَدَّ ٱلۡأَرۡضَ وَجَعَلَ فِيهَا رَوَٰسِيَ وَأَنۡهَٰرٗاۖ وَمِن كُلِّ ٱلثَّمَرَٰتِ جَعَلَ فِيهَا زَوۡجَيۡنِ ٱثۡنَيۡنِۖ يُغۡشِي ٱلَّيۡلَ ٱلنَّهَارَۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَتَفَكَّرُونَ

Ndipo Iye ndi Yemwe adatambasula nthaka ndikuika mapiri ndi mitsinje m’menemo. Ndipo mtundu uliwonse wazipatso adaupanga m’menemo kukhala mitundu iwiri iwiri, (yachimuna ndi yachikazi), amavindikira usiku ndi usana. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo (zazikulu zosonyeza kuti Allah alipo) kwa anthu olingalira. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 13

وَفِي ٱلۡأَرۡضِ قِطَعٞ مُّتَجَٰوِرَٰتٞ وَجَنَّٰتٞ مِّنۡ أَعۡنَٰبٖ وَزَرۡعٞ وَنَخِيلٞ صِنۡوَانٞ وَغَيۡرُ صِنۡوَانٖ يُسۡقَىٰ بِمَآءٖ وَٰحِدٖ وَنُفَضِّلُ بَعۡضَهَا عَلَىٰ بَعۡضٖ فِي ٱلۡأُكُلِۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ

Ndipo m’nthaka muli zigawo zogundana, (koma kumeretsa kwake kwa zomera nkosiyanasiyana). Mulinso minda ya mphesa ndi mmera wina ndi kanjedza wokhala ndi nthambi ndi wopanda nthambi; (zonsezi) zikuthiliridwa ndi madzi amodzi ofanana, ndipo tikuzichita zina kukhala zabwino kuposa zina mkakomedwe kake. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo kwa anthu anzeru. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 13

۞ وَإِن تَعۡجَبۡ فَعَجَبٞ قَوۡلُهُمۡ أَءِذَا كُنَّا تُرَٰبًا أَءِنَّا لَفِي خَلۡقٖ جَدِيدٍۗ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِرَبِّهِمۡۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡأَغۡلَٰلُ فِيٓ أَعۡنَاقِهِمۡۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Ndipo ngati ukudabwa, (basi) chodabwitsa kwambiri ndiko kuyankhula kwawo (koti): “Kodi tikadzakhala dothi, ndi zoona tidzakhala ndi chilengedwe chatsopano? (Allah sangathe zimenezi).” Iwowo ndi amene sadakhulupirire Mbuye wawo. Ndipo kwa iwowo mudzakhala magoli m’makosi mwawo; ndipo iwo ndi anthu a ku Moto, m’menemo adzakhala nthawi yaitali.[237] info

[237] Allah akuti chodabwitsa zedi kwa anthu osakhulupilira ndiko kunena kwawo kwakuti: “Kodi tikadzafa ndi kusanduka fumbi, tidzapatsidwanso moyo wina watsopano, zidzatheka bwanji zimenezi?” Ndithudi, kukana kwawo za kuuka kwa akufa nkododometsa pakuti amene adatha kulenga zinthu zikuluzikulu, monga thambo ndi nthaka, mitengo ndi zipatso, nyanja ndi mitsinje, ngokhoza kuwabweza pambuyo pa imfa yawo.

التفاسير: