Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - 齐切瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·白塔俩

An-Nâs

external-link copy
1 : 114

قُلۡ أَعُوذُ بِرَبِّ ٱلنَّاسِ

Nena: “Ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye (Mleri) wa anthu (Yemwe akulinganiza zinthu zawo).[503] info

[503] Allah pokhala Mlengi wa anthu ndi amenenso amawalera kuyambira pamene ali m’mimba mpaka kumapeto a moyo wawo pano pa dziko. Kuwaleraku kuli muuzimu, mthupi, mu mpweya, ndi pa chilichonse chofunika pa moyo wawo. Kuonjezera pa zimenezi adawapatsa nzeru ndi kuwasonyeza njira zabwino za dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo adawalamula kuzitsata njirazo. Adawasonyezanso njira zoipa za dziko lino lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo adawalamula kuti azipewe njira zoipazo.

التفاسير:

external-link copy
2 : 114

مَلِكِ ٱلنَّاسِ

Mfumu ya anthu ( Imene iri ndi mphamvu yochita chirichonse pa iwo). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 114

إِلَٰهِ ٱلنَّاسِ

Wopembedzedwa wa anthu. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 114

مِن شَرِّ ٱلۡوَسۡوَاسِ ٱلۡخَنَّاسِ

Kuzoipa za mnong’onezi (yemwe amathira unong’onezi wake m’mitimaya anthu) yemwenso amabisala (posiya unong’onezi wake ngati mwini mtimawo atankumbukira Allah).[504] info

[504] Mnong’onezi wa zoipa amene amabisala ndiye Satana, yemwe ntchito yake ndi kunong’oneza zoipa m’mitima ya anthu pofuna kuwasokeretsa ndi kuwaiwalitsa Allah. Koma akakumana ndi munthu wa chikhulupiliro cha mphamvu kapena yemwe amatamanda kwambiri Mbuye wake Allah, Satanayo amalephera ndipo amathawa; kubwerera m’mbuyo.

التفاسير:

external-link copy
5 : 114

ٱلَّذِي يُوَسۡوِسُ فِي صُدُورِ ٱلنَّاسِ

Yemwe amanong’oneza mzifuwa za anthu. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 114

مِنَ ٱلۡجِنَّةِ وَٱلنَّاسِ

Wochokera m’ziwanda ndi mwa anthu.”[505] info

[505] Mchiyankhulo cha Chiarabu aliyense woipitsitsa amatchedwa “shaitan” satana, munthu kapena chiwanda. Satana wa muwanthu ndiwoipitsitsa kwambiri kwa anthu kuposa wa m’ziwanda.

التفاسير: