[503] Allah pokhala Mlengi wa anthu ndi amenenso amawalera kuyambira pamene ali m’mimba mpaka kumapeto a moyo wawo pano pa dziko. Kuwaleraku kuli muuzimu, mthupi, mu mpweya, ndi pa chilichonse chofunika pa moyo wawo. Kuonjezera pa zimenezi adawapatsa nzeru ndi kuwasonyeza njira zabwino za dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo adawalamula kuzitsata njirazo. Adawasonyezanso njira zoipa za dziko lino lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo adawalamula kuti azipewe njira zoipazo.
[504] Mnong’onezi wa zoipa amene amabisala ndiye Satana, yemwe ntchito yake ndi kunong’oneza zoipa m’mitima ya anthu pofuna kuwasokeretsa ndi kuwaiwalitsa Allah. Koma akakumana ndi munthu wa chikhulupiliro cha mphamvu kapena yemwe amatamanda kwambiri Mbuye wake Allah, Satanayo amalephera ndipo amathawa; kubwerera m’mbuyo.