[15] Apa akunena kuti, “mfulu kwa mfulu” kuthanthauza kuti aliyense amene wapha nayenso aphedwe. Sikuti aphe munthu wina m’malo mwake.
Chisilamu chisanadze kudali kuponderezana zedi. Mfulu yochokera kufuko la pamwamba, ngati atapha mfulu yafuko la pansi eni a wakuphayo adali kukana kumpereka kuti aphedwe. M’malo mwake amapereka kapolo kuti ndiye aphedwe m’malo mwake. Kapolo wa mfulu wa fuko lapamwamba akapha kapolo wa mfulu wa fuko lapansi sadali kumpereka kuti akaphedwe. Amati: “Kapolo wathuyo ngwapamwamba pomwe wanuyo ngonyozeka. Choncho palibe kufanana pakati pa awiriwa.” Ndipo ngati zitachitika motere kuti kapolo wa onyozeka nkupha kapolo wa odzitukumula, odzitukumulawa amakana kupha kapolo uja m’malo mwake amafuna mfulu yochokera kufuko lonyozekalo. Tero Qur’ani idaletsa machitidwe oterewa. Anthu onse ngofanana, palibe kusiyana pakati pawo. Amene wapha aphedwe yemweyo osati wina, ngakhale atakhala mfulu kapena kapolo. Ili ndilo tanthauzo la Ayah (ndime) imeneyi.
Tsono gawo lina limene likuti: “Koma amene wakhululukidwa ndi m’bale wakeyo...” tanthauzo lake nkuti amene wamphera m’bale wake akamkhululukira wakuphayo amlipiritse dipo la ndalama. Tero apa akumuuza iyeyo kuti ngati atamkhululukira m’bale wakeyo nangomulipiritsa ndalama, alonjelere dipolo mwa ubwino. Nayenso wolipayo apereke mwa ubwino. Asachedwetse mwadala namzunguzazunguza. Tsono gawo lachitatu landime yokhayokhayi likutiuza za chifundo chimene Allah watichitira potilekera ife eni kusankha chiweruzo pankhaniyi.
Munthu yemwe amphera m’bale wake akhoza kuchita izi:
a) Kuliuza boma kuti liphenso yemwe adapha m’bale wakeyo.
b) Kapena kumlipiritsa dipo.
c) Kapena kumkhululukira popanda kulipa chilichonse. Ndipo gawo lomaliza landimeyi akumchenjeza wokhululukayo kuti asangomkhululukira munthuyo pamaso pa anthu kenako nkumuchita chiwembu mobisa.
[16] Muli moyo wabwino m’machitidwe abwino chifukwa chakuti potsata zimenezi aliyense adzakhala wotsata mwambo. Adzaopa kuti ngati apha mnzake nayenso aphedwa. Ngati achitira mnzake choipa nayenso amchitira choipa. Tero popewa zopwetekazo akhala ngati akusunga miyoyo ya anthu ena ndi wake womwe.
[17] Kale malamulo ogawira chuma cha masiye asanafotokozedwe adampatsa ufulu aliyense kuti alembe wasiya pa zachuma chakecho m’mene mwini angaonere. Wasiyawo ukhale m’njira ya chilungamo yolingana ndi Shariya. Asachite chinyengo cha mtundu uliwonse.
[18] Apa akuwachenjeza amene auzidwa wasiyawo kuti asasinthepo kanthu. Ndipo akunenetsa kuti ngati wasiyawo uwonongedwa ndiye kuti anthu omwe adalandira wasiyawo akhala ndi uchimo chifukwa chosintha wasiyawo. Koma ngati wasiyawo udalembedwa mopanda chilungamo, monga kuti iye adati: “Chuma changa m’dzawapatse ana anga aamuna okha basi,” nkusiya kutchulapo aakazi, apo Allah akuloleza olandira wasiyawo kuti aukonze ndi kuwagawira ana onsewo mwachilungamo.