[22] Pachiyambi pomwe lamulo la kusala lidakhazikitsidwa adawaletsa anthu kukumana ndi akazi awo usiku pambuyo poti iwo agona tulo ngakhale kuti angogona pang’ono pokha. Kukumana ndi mkazi akumane asanagone. Tero lamuloli lidali lovuta kwambiri kwa iwo kulitsata. Ena a iwo adalakwa pang’ono. Choncho kudalengezedwa kuti: “Tsopano pali chilolezo choti akhoza kuchita chilichonse mpaka m’bandakucha. Ndipo kunena koti: “Funani chimene Allah wakulamulani”, ndikulilimbikitsa lamulo kuchilolezocho. Musati kuti poti kale adakuletsani kukumana ndi akazi anu pambuyo pogona tulo ndiye mupitirize kutero - iyayi. Koma tsatirani chilolezocho.
“Itikafu” ndikuchita chitsimikizo munthu chokhala mu msikiti kwamasiku akutiakuti kapena nthawi yakutiyakuti. Ndipo pempheroli limachitika nthawi zambiri m’mwezi wa Ramadan. Akachita chitsimikizocho (niya) saloledwa kutuluka mu msikitimo pokhapokha patakhala chifukwa chachikulu chotulukira, monga kupita kukadzithandiza.
[23] M’nthawi ya umbuli anthu ankati akalowa m’mapemphero a Hajj sadali kulowa m’nyumba zawo podzera pakhomo pa nyumba. Ndipo sadalinso kutulukira pakhomo koma amaboola chibowo kuseri kwa nyumba nkumalowerapo ndi kutulukirapo namaganiza kuti kutero ndimapemphero okondweretsa Allah. Tsono apa Allah akuletsa mchitidwe umenewo.
[24] lyi ndi imodzi mwa ndime zomwe zikufotokoza bodza la amene akunena kuti chisilamu chidafala ndi lupanga powathira anthu nkhondo mowakakamiza kuti alowe m’Chisilamu.
Limeneli, ndithu ndibodza lamkunkhuniza. Apa pakuonetsa kuti Allah akuwapatsa chilolezo asilamu kuti amenyane ndi amene akuwaputa. Palibe chilolezo kwa iwo chowamenyera anthu osawaputa.