Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - Çevaca Tercüme - Halid İbrahim Pitala

Sayfa numarası:close

external-link copy
177 : 2

۞ لَّيۡسَ ٱلۡبِرَّ أَن تُوَلُّواْ وُجُوهَكُمۡ قِبَلَ ٱلۡمَشۡرِقِ وَٱلۡمَغۡرِبِ وَلَٰكِنَّ ٱلۡبِرَّ مَنۡ ءَامَنَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ وَٱلۡكِتَٰبِ وَٱلنَّبِيِّـۧنَ وَءَاتَى ٱلۡمَالَ عَلَىٰ حُبِّهِۦ ذَوِي ٱلۡقُرۡبَىٰ وَٱلۡيَتَٰمَىٰ وَٱلۡمَسَٰكِينَ وَٱبۡنَ ٱلسَّبِيلِ وَٱلسَّآئِلِينَ وَفِي ٱلرِّقَابِ وَأَقَامَ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتَى ٱلزَّكَوٰةَ وَٱلۡمُوفُونَ بِعَهۡدِهِمۡ إِذَا عَٰهَدُواْۖ وَٱلصَّٰبِرِينَ فِي ٱلۡبَأۡسَآءِ وَٱلضَّرَّآءِ وَحِينَ ٱلۡبَأۡسِۗ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ صَدَقُواْۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُتَّقُونَ

Ubwino suli potembenuzira nkhope zanu mbali yakuvuma ndi kuzambwe (popemphera Swala); koma ubwino weniweni ndi (wa omwe) akukhulupirira Allah, tsiku lachimaliziro, angelo, buku ndi aneneri; napereka chuma - uku eni akuchifunabe - kwa achibale ndi amasiye, ndi masikini ndi a paulendo (omwe alibe choyendera), ndi opempha, ndi kuombolera akapolo; napemphera Swala, napereka chopereka (Zakaat); ndi okwaniritsa malonjezo awo akalonjeza, ndi opirira ndi umphawi ndi matenda ndi panthawi yankhondo. Iwowo ndi amene atsimikiza (Chisilamu chawo). Ndiponso iwowo ndi omwe ali oopa Allah. info
التفاسير:

external-link copy
178 : 2

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُتِبَ عَلَيۡكُمُ ٱلۡقِصَاصُ فِي ٱلۡقَتۡلَىۖ ٱلۡحُرُّ بِٱلۡحُرِّ وَٱلۡعَبۡدُ بِٱلۡعَبۡدِ وَٱلۡأُنثَىٰ بِٱلۡأُنثَىٰۚ فَمَنۡ عُفِيَ لَهُۥ مِنۡ أَخِيهِ شَيۡءٞ فَٱتِّبَاعُۢ بِٱلۡمَعۡرُوفِ وَأَدَآءٌ إِلَيۡهِ بِإِحۡسَٰنٖۗ ذَٰلِكَ تَخۡفِيفٞ مِّن رَّبِّكُمۡ وَرَحۡمَةٞۗ فَمَنِ ٱعۡتَدَىٰ بَعۡدَ ذَٰلِكَ فَلَهُۥ عَذَابٌ أَلِيمٞ

E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu Qiswas (kubwezerana) molingana kwa ophedwa; mfulu kwa mfulu, kapolo kwa kapolo, mkazi kwa mkazi. Koma amene wakhululukidwa ndi m’bale wakeyo pa chinthu Chilichonse, atsatire ndi kulonjelera dipolo mwaubwino. (Nayenso wolipa) apereke kwa iye mwa ubwino. Kumeneko ndikufewetsa kumene kwachokera kwa Mbuye wanu, ndiponso chifundo. Ndipo amene alumphe malire pambuyo pa izi, iye adzapeza chilango chopweteka.[15] info

[15] Apa akunena kuti, “mfulu kwa mfulu” kuthanthauza kuti aliyense amene wapha nayenso aphedwe. Sikuti aphe munthu wina m’malo mwake.
Chisilamu chisanadze kudali kuponderezana zedi. Mfulu yochokera kufuko la pamwamba, ngati atapha mfulu yafuko la pansi eni a wakuphayo adali kukana kumpereka kuti aphedwe. M’malo mwake amapereka kapolo kuti ndiye aphedwe m’malo mwake. Kapolo wa mfulu wa fuko lapamwamba akapha kapolo wa mfulu wa fuko lapansi sadali kumpereka kuti akaphedwe. Amati: “Kapolo wathuyo ngwapamwamba pomwe wanuyo ngonyozeka. Choncho palibe kufanana pakati pa awiriwa.” Ndipo ngati zitachitika motere kuti kapolo wa onyozeka nkupha kapolo wa odzitukumula, odzitukumulawa amakana kupha kapolo uja m’malo mwake amafuna mfulu yochokera kufuko lonyozekalo. Tero Qur’ani idaletsa machitidwe oterewa. Anthu onse ngofanana, palibe kusiyana pakati pawo. Amene wapha aphedwe yemweyo osati wina, ngakhale atakhala mfulu kapena kapolo. Ili ndilo tanthauzo la Ayah (ndime) imeneyi.
Tsono gawo lina limene likuti: “Koma amene wakhululukidwa ndi m’bale wakeyo...” tanthauzo lake nkuti amene wamphera m’bale wake akamkhululukira wakuphayo amlipiritse dipo la ndalama. Tero apa akumuuza iyeyo kuti ngati atamkhululukira m’bale wakeyo nangomulipiritsa ndalama, alonjelere dipolo mwa ubwino. Nayenso wolipayo apereke mwa ubwino. Asachedwetse mwadala namzunguzazunguza. Tsono gawo lachitatu landime yokhayokhayi likutiuza za chifundo chimene Allah watichitira potilekera ife eni kusankha chiweruzo pankhaniyi.
Munthu yemwe amphera m’bale wake akhoza kuchita izi:
a) Kuliuza boma kuti liphenso yemwe adapha m’bale wakeyo.
b) Kapena kumlipiritsa dipo.
c) Kapena kumkhululukira popanda kulipa chilichonse. Ndipo gawo lomaliza landimeyi akumchenjeza wokhululukayo kuti asangomkhululukira munthuyo pamaso pa anthu kenako nkumuchita chiwembu mobisa.

التفاسير:

external-link copy
179 : 2

وَلَكُمۡ فِي ٱلۡقِصَاصِ حَيَوٰةٞ يَٰٓأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ

Mu Qiswas (kubwezerana kofanana) muli kusunga moyo kwa inu, E, inu eni nzeru! Kuti mudzitchinjirize (ku mchitidwe ophana).[16] info

[16] Muli moyo wabwino m’machitidwe abwino chifukwa chakuti potsata zimenezi aliyense adzakhala wotsata mwambo. Adzaopa kuti ngati apha mnzake nayenso aphedwa. Ngati achitira mnzake choipa nayenso amchitira choipa. Tero popewa zopwetekazo akhala ngati akusunga miyoyo ya anthu ena ndi wake womwe.

التفاسير:

external-link copy
180 : 2

كُتِبَ عَلَيۡكُمۡ إِذَا حَضَرَ أَحَدَكُمُ ٱلۡمَوۡتُ إِن تَرَكَ خَيۡرًا ٱلۡوَصِيَّةُ لِلۡوَٰلِدَيۡنِ وَٱلۡأَقۡرَبِينَ بِٱلۡمَعۡرُوفِۖ حَقًّا عَلَى ٱلۡمُتَّقِينَ

Kwalamulidwa kwa inu kuti mmodzi wanu imfa ikamuyandikira, ngati asiya chuma, apereke malangizo (pa zachumacho) kwa makolo ake awiri ndi achibale ake, mwa ubwino. Ichi nchilamulo kwa oopa Allah.[17] info

[17] Kale malamulo ogawira chuma cha masiye asanafotokozedwe adampatsa ufulu aliyense kuti alembe wasiya pa zachuma chakecho m’mene mwini angaonere. Wasiyawo ukhale m’njira ya chilungamo yolingana ndi Shariya. Asachite chinyengo cha mtundu uliwonse.

التفاسير:

external-link copy
181 : 2

فَمَنۢ بَدَّلَهُۥ بَعۡدَ مَا سَمِعَهُۥ فَإِنَّمَآ إِثۡمُهُۥ عَلَى ٱلَّذِينَ يُبَدِّلُونَهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٞ

Ndipo amene asinthe malangizowo pambuyo pakuwamva; uchimo wake uli pa amene akusinthawo. Ndithudi, Allah Ngwakumva; Ngodziwa.[18] info

[18] Apa akuwachenjeza amene auzidwa wasiyawo kuti asasinthepo kanthu. Ndipo akunenetsa kuti ngati wasiyawo uwonongedwa ndiye kuti anthu omwe adalandira wasiyawo akhala ndi uchimo chifukwa chosintha wasiyawo. Koma ngati wasiyawo udalembedwa mopanda chilungamo, monga kuti iye adati: “Chuma changa m’dzawapatse ana anga aamuna okha basi,” nkusiya kutchulapo aakazi, apo Allah akuloleza olandira wasiyawo kuti aukonze ndi kuwagawira ana onsewo mwachilungamo.

التفاسير: