[318] Pamene Mtumiki (s.a.w) adali mu mzinda wa Madina adamzinga magulu ambiri a nkhondo omwe ena a iwo adali a mtundu wa Ghatfan, Ayuda a Chikuraidha ndi Ayuda a Bani Nadhir. Adali ochuluka 12,000.
Pamene Mtumiki (s.a.w) adamva za kudza kwawo adakumba chidzenje chachikulu kumbali ina ya mzinda wa Madina yomwe adaiganizira kuti adani angalowereko. Izi zidachitika potsatira malangizo a Salman Farisiyu. Kenako Mtumiki (s.a.w) adatuluka ndi ankhondo ake okwana 3,000 nakamanga mahema awo pafupi ndi chidzenjecho moyang’anizana ndi adani awo. Asilamu adagwidwa ndi mantha aakulu kotero kuti achiphamaso adayamba kuthawa. Koma pompo Allah adatumizira adaniwo chimphepo ndi magulu a nkhondo a angelo omwe sadathe kuwaona ndi maso awo, nawabalalitsa adaniwo ndi kuwatayira katundu wawo kutali.