क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला

पृष्ठ संख्या:close

external-link copy
7 : 33

وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِنَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ مِيثَٰقَهُمۡ وَمِنكَ وَمِن نُّوحٖ وَإِبۡرَٰهِيمَ وَمُوسَىٰ وَعِيسَى ٱبۡنِ مَرۡيَمَۖ وَأَخَذۡنَا مِنۡهُم مِّيثَٰقًا غَلِيظٗا

Ndipo (akumbutse) pamene tidalandira kuchokera kwa Aneneri onse pangano lawo. Ndi kwa iwe, ndi kwa Nuh, Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Ndipo tidatenga kwa iwo pangano lamphamvu (kuti adzafikitsa uthenga wa Allah kwa anthu ndi kuitanira anthu ku chipembedzo cha Allah). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 33

لِّيَسۡـَٔلَ ٱلصَّٰدِقِينَ عَن صِدۡقِهِمۡۚ وَأَعَدَّ لِلۡكَٰفِرِينَ عَذَابًا أَلِيمٗا

Kuti (Allah) adzafunse owona (aneneri) (tsiku la chimaliziro) pa zimene adanena (kwa anthu awo zakufikitsa uthenga woonadi kwa iwo). Ndipo Allah wawakonzera (osakhulupirira) chilango chopweteka. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 33

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ إِذۡ جَآءَتۡكُمۡ جُنُودٞ فَأَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ رِيحٗا وَجُنُودٗا لَّمۡ تَرَوۡهَاۚ وَكَانَ ٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرًا

E inu amene mwakhulupirira! Kumbukirani chisomo cha Allah chimene chili pa inu, pamene adakudzerani magulu a nkhondo. Ndipo tidawatumizira mphepo ndi magulu a nkhondo (a angelo) amene simudawaone. Ndipo Allah akuona (zonse) zimene mukuchita.[318] info

[318] Pamene Mtumiki (s.a.w) adali mu mzinda wa Madina adamzinga magulu ambiri a nkhondo omwe ena a iwo adali a mtundu wa Ghatfan, Ayuda a Chikuraidha ndi Ayuda a Bani Nadhir. Adali ochuluka 12,000.
Pamene Mtumiki (s.a.w) adamva za kudza kwawo adakumba chidzenje chachikulu kumbali ina ya mzinda wa Madina yomwe adaiganizira kuti adani angalowereko. Izi zidachitika potsatira malangizo a Salman Farisiyu. Kenako Mtumiki (s.a.w) adatuluka ndi ankhondo ake okwana 3,000 nakamanga mahema awo pafupi ndi chidzenjecho moyang’anizana ndi adani awo. Asilamu adagwidwa ndi mantha aakulu kotero kuti achiphamaso adayamba kuthawa. Koma pompo Allah adatumizira adaniwo chimphepo ndi magulu a nkhondo a angelo omwe sadathe kuwaona ndi maso awo, nawabalalitsa adaniwo ndi kuwatayira katundu wawo kutali.

التفاسير:

external-link copy
10 : 33

إِذۡ جَآءُوكُم مِّن فَوۡقِكُمۡ وَمِنۡ أَسۡفَلَ مِنكُمۡ وَإِذۡ زَاغَتِ ٱلۡأَبۡصَٰرُ وَبَلَغَتِ ٱلۡقُلُوبُ ٱلۡحَنَاجِرَ وَتَظُنُّونَ بِٱللَّهِ ٱلظُّنُونَا۠

Pamene adakudzerani cha kumtunda kwanu, ndi kunsi kwanu (kumtunda kwa dambo ndi kumunsi kwake), pamene maso adangoti tong’oo chammbali ndipo mitima idafika kum’mero (chifukwa cha mantha ndi kunjenjemera) uku mukumganizira Allah maganizo osiyanasiyana. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 33

هُنَالِكَ ٱبۡتُلِيَ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ وَزُلۡزِلُواْ زِلۡزَالٗا شَدِيدٗا

Panthawi imeneyo okhulupirira adayesedwa mayeso aakulu. Adanjenjemeretsedwa kunjenjemera kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 33

وَإِذۡ يَقُولُ ٱلۡمُنَٰفِقُونَ وَٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ مَّا وَعَدَنَا ٱللَّهُ وَرَسُولُهُۥٓ إِلَّا غُرُورٗا

Ndipo pamene ankanena achiphamaso (achinyengo) ndi omwe m’mitima mwawo muli matenda: “Palibe chomwe adatilonjeza Allah ndi Mtumiki Wake koma chinyengo basi.” info
التفاسير:

external-link copy
13 : 33

وَإِذۡ قَالَت طَّآئِفَةٞ مِّنۡهُمۡ يَٰٓأَهۡلَ يَثۡرِبَ لَا مُقَامَ لَكُمۡ فَٱرۡجِعُواْۚ وَيَسۡتَـٔۡذِنُ فَرِيقٞ مِّنۡهُمُ ٱلنَّبِيَّ يَقُولُونَ إِنَّ بُيُوتَنَا عَوۡرَةٞ وَمَا هِيَ بِعَوۡرَةٍۖ إِن يُرِيدُونَ إِلَّا فِرَارٗا

Ndipo pamene gulu lina mwa iwo lidanena: “E inu nzika za mu Yathiriba (Madina)! Palibe njira kwa inu yokhalira (pa nkhondo yogonjayi). Choncho bwererani (ku nyumba zanu; msiyeni Muhammad alimbane yekha ndi adani ake).” Ndipo gulu lina la nkhondo lochokera mwa iwo limapempha chilolezo kwa Mneneri (s.a.w) ( chobwelera ku Madina) ponena (kuti): “Ndithu nyumba zathu nzamaliseche (zopanda chitetezo).” Koma izo sizamaliseche. Sakufuna china, koma kuthawa basi. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 33

وَلَوۡ دُخِلَتۡ عَلَيۡهِم مِّنۡ أَقۡطَارِهَا ثُمَّ سُئِلُواْ ٱلۡفِتۡنَةَ لَأٓتَوۡهَا وَمَا تَلَبَّثُواْ بِهَآ إِلَّا يَسِيرٗا

Ndipo akadawalowera (magulu ankhondo a adaniwo), mbali zonse (za Mzindawo), kenako nkupemphedwa kuti atuluke m’Chisilamu ndi kumenyana ndi Asilamu, akadachita zimenezo; ndipo sakadayembekezera koma nthawi yochepa basi. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 33

وَلَقَدۡ كَانُواْ عَٰهَدُواْ ٱللَّهَ مِن قَبۡلُ لَا يُوَلُّونَ ٱلۡأَدۡبَٰرَۚ وَكَانَ عَهۡدُ ٱللَّهِ مَسۡـُٔولٗا

Ndipo ndithu (awa amene adathawa pabwalo la nkhondo), adali atamulonjeza kale Allah (kuti iwo) sadzatembenuza misana (kuthawa). Ndipo lonjezo la Allah nlofunsidwa. (Choncho iwo adzafunsidwa pa zomwe adalonjeza kwa Allah). info
التفاسير: