قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

بەت نومۇرى:close

external-link copy
31 : 33

۞ وَمَن يَقۡنُتۡ مِنكُنَّ لِلَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَتَعۡمَلۡ صَٰلِحٗا نُّؤۡتِهَآ أَجۡرَهَا مَرَّتَيۡنِ وَأَعۡتَدۡنَا لَهَا رِزۡقٗا كَرِيمٗا

۞ Koma yense mwa inu amene amvere Allah ndi Mneneri Wake, ndi kumachita zabwino, timpatsa malipiro ake kawiri ndi kumkonzera rizq laulemu. info
التفاسير:

external-link copy
32 : 33

يَٰنِسَآءَ ٱلنَّبِيِّ لَسۡتُنَّ كَأَحَدٖ مِّنَ ٱلنِّسَآءِ إِنِ ٱتَّقَيۡتُنَّۚ فَلَا تَخۡضَعۡنَ بِٱلۡقَوۡلِ فَيَطۡمَعَ ٱلَّذِي فِي قَلۡبِهِۦ مَرَضٞ وَقُلۡنَ قَوۡلٗا مَّعۡرُوفٗا

E inu akazi a Mneneri! Inu simuli monga mmodzi wa akazi ena (omwe siakazi a Mtumiki, paulemelero) ngati muopa Allah. Choncho musalobodole mawu (mowakometsa poyankhulana ndi amuna,) kuti asalakelake (kuchita zoipa ndi inu) yemwe mu mtima mwake muli matenda (achiwerewere). Koma nenani zonena zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
33 : 33

وَقَرۡنَ فِي بُيُوتِكُنَّ وَلَا تَبَرَّجۡنَ تَبَرُّجَ ٱلۡجَٰهِلِيَّةِ ٱلۡأُولَىٰۖ وَأَقِمۡنَ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتِينَ ٱلزَّكَوٰةَ وَأَطِعۡنَ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥٓۚ إِنَّمَا يُرِيدُ ٱللَّهُ لِيُذۡهِبَ عَنكُمُ ٱلرِّجۡسَ أَهۡلَ ٱلۡبَيۡتِ وَيُطَهِّرَكُمۡ تَطۡهِيرٗا

Ndipo khalani mnyumba zanu, ndipo musadzionetsere (kwa amuna) uku mutadzikongoletsa monga mmene ankaonetsera zokongoletsa zawo (akazi) a m’nthawi ya umbuli wakale. Ndipo pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat, mverani Allah ndi Mtumiki Wake. Ndithu Allah akufuna kukuchotserani uve e, inu a kunyumba (ya Mneneri)! Ndi kuti akuyeretseni ndithu. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 33

وَٱذۡكُرۡنَ مَا يُتۡلَىٰ فِي بُيُوتِكُنَّ مِنۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ وَٱلۡحِكۡمَةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ لَطِيفًا خَبِيرًا

Ndipo lowezani pamtima zimene zikunenedwa m’nyumba zanu; ndime za mawu a Allah ndi (zonena za Mtumiki) zanzeru. Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika kwambiri, ndi zapoyera. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 33

إِنَّ ٱلۡمُسۡلِمِينَ وَٱلۡمُسۡلِمَٰتِ وَٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ وَٱلۡقَٰنِتِينَ وَٱلۡقَٰنِتَٰتِ وَٱلصَّٰدِقِينَ وَٱلصَّٰدِقَٰتِ وَٱلصَّٰبِرِينَ وَٱلصَّٰبِرَٰتِ وَٱلۡخَٰشِعِينَ وَٱلۡخَٰشِعَٰتِ وَٱلۡمُتَصَدِّقِينَ وَٱلۡمُتَصَدِّقَٰتِ وَٱلصَّٰٓئِمِينَ وَٱلصَّٰٓئِمَٰتِ وَٱلۡحَٰفِظِينَ فُرُوجَهُمۡ وَٱلۡحَٰفِظَٰتِ وَٱلذَّٰكِرِينَ ٱللَّهَ كَثِيرٗا وَٱلذَّٰكِرَٰتِ أَعَدَّ ٱللَّهُ لَهُم مَّغۡفِرَةٗ وَأَجۡرًا عَظِيمٗا

Ndithu Asilamu achimuna ndi Asilamu achikazi; okhulupirira achimuna ndi okhulupirira achikazi; omvera achimuna ndi omvera achikazi; owona achimuna ndi owona achikazi; opirira achimuna ndi opirira achikazi; odzichepetsa achimuna ndi odzichepetsa achikazi; opereka sadaka achimuna ndi opereka sadaka achikazi; osala achimuna ndi osala achikazi; osunga umaliseche wawo (kuchiwerewere) achimuna ndi osunga umaliseche wawo achikazi; otamanda Allah kwambiri achimuna ndi otamanda Allah kwambiri achikazi, Allah wawakonzera chikhululuko ndi malipiro aakulu. info
التفاسير: