แปล​ความหมาย​อัลกุรอาน​ - คำแปลภาษาชิเชวา - โดยคอลิด อิบรอฮีม เบตาลา

Al-Fajr

external-link copy
1 : 89

وَٱلۡفَجۡرِ

Ndikulumbilira kuyera kwa m’bandakucha; (pamene usiku uthawa). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 89

وَلَيَالٍ عَشۡرٖ

Ndi masiku khumi (a mwezi wa Dhul-Hijjah omwe ngopatulika kwa Allah).[430] info

[430] Tanthauzo la Ayah iyi ndi masiku khumi olemekezeka omwe ali mkhumi loyamba la mwezi wa Thul-Hijjah umene ndi mwezi wa 12 pa kalendala ya Chisilamu. Amenewa ndi masiku olemekezeka kuposa masiku onse ngakhale masiku a Ramadan kupatula usiku wa LAILA-TUL-QADR, ndi masiku khumi omaliza a mwezi wa Ramadan. Choncho ndi bwino kuchulukitsa mapemphero m’masiku amenewa.

التفاسير:

external-link copy
3 : 89

وَٱلشَّفۡعِ وَٱلۡوَتۡرِ

Ndi Shaf’i ndi Witri: (nambala yogawika ndi yosagawika).[431] info

[431] Shafi ndi nambala yotheka kugawa ndi 2 (even number) Witri ndi nambala yosatheka kuigawa ndi 2 (odd number). Cholinga cha Allah pamenepa ndi kuzilumbilira zinthu zonse zimene adazilenga, zowerengedwa mnjira zonse ziwiri.

التفاسير:

external-link copy
4 : 89

وَٱلَّيۡلِ إِذَا يَسۡرِ

Ndi usiku pamene ukupita (chifukwa cha kuyenda kwa dziko kodabwitsa). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 89

هَلۡ فِي ذَٰلِكَ قَسَمٞ لِّذِي حِجۡرٍ

Kodi m’zimene zatchulidwazi simuli kulumbira kokwanira, kwa munthu wa nzeru? info
التفاسير:

external-link copy
6 : 89

أَلَمۡ تَرَ كَيۡفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِعَادٍ

Kodi sudadziwe momwe Mbuye wako adawalangira Âdi (anthu a mneneri Hûd). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 89

إِرَمَ ذَاتِ ٱلۡعِمَادِ

Aku Irama; ataliatali ngati zipilala.[432] info

[432] (Ndime 7-9) Âdi aku Irama ndi mtundu wa Mneneri Hud. Adali akuluakulu matupi a mphamvu kwambiri mwakuti ankanena kuti: “Ndani wamphamvu kuposa ife!” Thamudu (Samudu) ndi mtundu wa Mneneri Swaleh. Iwowa adali kukhala ku mpoto kwa chilumba cha Arabia.

التفاسير:

external-link copy
8 : 89

ٱلَّتِي لَمۡ يُخۡلَقۡ مِثۡلُهَا فِي ٱلۡبِلَٰدِ

Omwe onga iwo sadalengedwe m’maiko ena? info
التفاسير:

external-link copy
9 : 89

وَثَمُودَ ٱلَّذِينَ جَابُواْ ٱلصَّخۡرَ بِٱلۡوَادِ

Ndi Asamudu, (anthu a mneneri Swaleh) amene adali kudula matanthwe ku chigwa (chotchedwa Wadi Qura ndi kumamanga nyumba zikuluzikulu)? info
التفاسير:

external-link copy
10 : 89

وَفِرۡعَوۡنَ ذِي ٱلۡأَوۡتَادِ

Komanso Firiauna (Farawo) mwini magulu ankhondo (omwe amalimbikitsa ufumu wake monga momwe zichiri zimalimbikitsira tenti)? info
التفاسير:

external-link copy
11 : 89

ٱلَّذِينَ طَغَوۡاْ فِي ٱلۡبِلَٰدِ

Amene adaipitsa m’maiko mopyola malire? info
التفاسير:

external-link copy
12 : 89

فَأَكۡثَرُواْ فِيهَا ٱلۡفَسَادَ

Ndipo adachulukitsa m’menemo kuononga (pamwamba pa kuononga).[433] info

[433] Mzinthu zoipa zimene Farawo adachita, ndi kudzitcha kuti iye ndi mulungu, kupha ana achimuna popanda chilungamo, ndi kuwazunza Aisraeli.

التفاسير:

external-link copy
13 : 89

فَصَبَّ عَلَيۡهِمۡ رَبُّكَ سَوۡطَ عَذَابٍ

Choncho Mbuye wako adawathira ndi mitundu ya zilango (zoopsa). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 89

إِنَّ رَبَّكَ لَبِٱلۡمِرۡصَادِ

Ndithu Mbuye wako ali tcheru (ndi zochita za anthu. Ndipo akuwasungira kuti adzawalipire).[434] info

[434] Apa ndikuti Allah akuwaona anthu Ake nthawi ili yonse. Palibe chimene iwo achita popanda Iye kuchiona ndi kuchilemba.

التفاسير:

external-link copy
15 : 89

فَأَمَّا ٱلۡإِنسَٰنُ إِذَا مَا ٱبۡتَلَىٰهُ رَبُّهُۥ فَأَكۡرَمَهُۥ وَنَعَّمَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّيٓ أَكۡرَمَنِ

Pamene munthu Mbuye wake akumuyesa (mayeso) ndikumulemekeza ndi kumpatsa mtendere (wachuma, ulemelero ndi mphamvu) amanena monyada: Mbuye wanga wandilemekeza (chifukwa zimenezi nzondiyenera ine). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 89

وَأَمَّآ إِذَا مَا ٱبۡتَلَىٰهُ فَقَدَرَ عَلَيۡهِ رِزۡقَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّيٓ أَهَٰنَنِ

Koma akamuyesa mayeso ndi kumchepetsera rizq lake, (chuma) amanena (motaya rntima): Mbuye wanga wandinyoza! info
التفاسير:

external-link copy
17 : 89

كَلَّاۖ بَل لَّا تُكۡرِمُونَ ٱلۡيَتِيمَ

Sichoncho ayi, (monga momwe mukuganizira) koma inu simuchitira za ufulu ana amasiye! info
التفاسير:

external-link copy
18 : 89

وَلَا تَحَٰٓضُّونَ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ

Ndipo simulimbikitsana za kudyetsa osauka, info
التفاسير:

external-link copy
19 : 89

وَتَأۡكُلُونَ ٱلتُّرَاثَ أَكۡلٗا لَّمّٗا

Ndipo mukudya chuma cha masiye; kudya kosusuka.[435] info

[435] Arabu asadalowe m’Chisilamu akazi sadali kugawiridwa chuma cha masiye kudzanso ana aang’onoang’ono a masiye sadali kuchiona chumacho.

التفاسير:

external-link copy
20 : 89

وَتُحِبُّونَ ٱلۡمَالَ حُبّٗا جَمّٗا

Ndiponso mukukonda chuma; kukonda kopyola muyeso. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 89

كَلَّآۖ إِذَا دُكَّتِ ٱلۡأَرۡضُ دَكّٗا دَكّٗا

Sichoncho! (Siyani machitidwe amenewa); nthaka ikadzapondedwa (ndikuifafaniza). info
التفاسير:

external-link copy
22 : 89

وَجَآءَ رَبُّكَ وَٱلۡمَلَكُ صَفّٗا صَفّٗا

Ndikubwera Mbuye wako (mmabweredwe omwe akuwadziwa Iye Mwini) ndi angelo ali mmizeremizere. info
التفاسير:

external-link copy
23 : 89

وَجِاْيٓءَ يَوۡمَئِذِۭ بِجَهَنَّمَۚ يَوۡمَئِذٖ يَتَذَكَّرُ ٱلۡإِنسَٰنُ وَأَنَّىٰ لَهُ ٱلذِّكۡرَىٰ

Ndi kubweretsedwa Jahannam pa tsikulo, basi tsiku limenelo munthu adzakumbukira, koma kukumbuka kumeneko kudzamthandiza chiyani? info
التفاسير:

external-link copy
24 : 89

يَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي قَدَّمۡتُ لِحَيَاتِي

Adzanena: Kalanga ine! Ndikadatsogoza zabwino pa za moyo wanga uno! info
التفاسير:

external-link copy
25 : 89

فَيَوۡمَئِذٖ لَّا يُعَذِّبُ عَذَابَهُۥٓ أَحَدٞ

Motero patsikuli, palibe wina amene adzalange monga momwe (Allah) adzalangire.[436] info

[436] (Ndime 25-26) Tanthauzo lake ndikuti palibe chofanizira chilango cha Allah chomwe chidzaperekedwe kwa akafiri ndiponso ndi kunjata komwe akafiri adzanjatidwe.

التفاسير:

external-link copy
26 : 89

وَلَا يُوثِقُ وَثَاقَهُۥٓ أَحَدٞ

Ndiponso sanganjate aliyense monga kunjata kwa iye (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
27 : 89

يَٰٓأَيَّتُهَا ٱلنَّفۡسُ ٱلۡمُطۡمَئِنَّةُ

E iwe mzimu wokhazikika (ndi choona)![437] info

[437] “Mzimu wokhazikika” ndi mzimu wa munthu wokhulupilira amene akuchita zomwe walamulidwa ndi kusiya zimene waletsedwa. Umenewo ndiwo mzimu umene udzakhale wodekha pa tsiku lachimaliziro chifukwa chakuti pa tsikulo sudzakhala ndi mantha kapena kudandaula.

التفاسير:

external-link copy
28 : 89

ٱرۡجِعِيٓ إِلَىٰ رَبِّكِ رَاضِيَةٗ مَّرۡضِيَّةٗ

Bwerera kwa Mbuye wako uli wokondwera (ndi zomwe wapatsidwa), ndipo uli woyanjidwa (ndi Allah pa zomwe udatsogoza).[438] info

[438] Tanthauzo lake nkuti mzimu wokhazikika udzakondwera ndi zimene udzalandira kwa Allah tsiku limenelo ndipo naye Allah adzakondwera nawo.

التفاسير:

external-link copy
29 : 89

فَٱدۡخُلِي فِي عِبَٰدِي

Lowa mgulu la akapolo anga abwino. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 89

وَٱدۡخُلِي جَنَّتِي

Ndipo lowa m’munda Wanga (mnyumba ya mtendere wa muyaya). info
التفاسير: