[430] Tanthauzo la Ayah iyi ndi masiku khumi olemekezeka omwe ali mkhumi loyamba la mwezi wa Thul-Hijjah umene ndi mwezi wa 12 pa kalendala ya Chisilamu. Amenewa ndi masiku olemekezeka kuposa masiku onse ngakhale masiku a Ramadan kupatula usiku wa LAILA-TUL-QADR, ndi masiku khumi omaliza a mwezi wa Ramadan. Choncho ndi bwino kuchulukitsa mapemphero m’masiku amenewa.
[431] Shafi ndi nambala yotheka kugawa ndi 2 (even number) Witri ndi nambala yosatheka kuigawa ndi 2 (odd number). Cholinga cha Allah pamenepa ndi kuzilumbilira zinthu zonse zimene adazilenga, zowerengedwa mnjira zonse ziwiri.
[432] (Ndime 7-9) Âdi aku Irama ndi mtundu wa Mneneri Hud. Adali akuluakulu matupi a mphamvu kwambiri mwakuti ankanena kuti: “Ndani wamphamvu kuposa ife!” Thamudu (Samudu) ndi mtundu wa Mneneri Swaleh. Iwowa adali kukhala ku mpoto kwa chilumba cha Arabia.
[436] (Ndime 25-26) Tanthauzo lake ndikuti palibe chofanizira chilango cha Allah chomwe chidzaperekedwe kwa akafiri ndiponso ndi kunjata komwe akafiri adzanjatidwe.
[437] “Mzimu wokhazikika” ndi mzimu wa munthu wokhulupilira amene akuchita zomwe walamulidwa ndi kusiya zimene waletsedwa. Umenewo ndiwo mzimu umene udzakhale wodekha pa tsiku lachimaliziro chifukwa chakuti pa tsikulo sudzakhala ndi mantha kapena kudandaula.
[438] Tanthauzo lake nkuti mzimu wokhazikika udzakondwera ndi zimene udzalandira kwa Allah tsiku limenelo ndipo naye Allah adzakondwera nawo.