ශුද්ධවූ අල් කුර්ආන් අර්ථ කථනය - චිචේවා පරිවර්තනය - කාලිද් ඉබ්රාහීම් බීතාලා

පිටු අංක:close

external-link copy
155 : 4

فَبِمَا نَقۡضِهِم مِّيثَٰقَهُمۡ وَكُفۡرِهِم بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَقَتۡلِهِمُ ٱلۡأَنۢبِيَآءَ بِغَيۡرِ حَقّٖ وَقَوۡلِهِمۡ قُلُوبُنَا غُلۡفُۢۚ بَلۡ طَبَعَ ٱللَّهُ عَلَيۡهَا بِكُفۡرِهِمۡ فَلَا يُؤۡمِنُونَ إِلَّا قَلِيلٗا

Choncho (tidawalanga) chifukwa chakuswa mapangano awo, ndi kukana kwawo zisonyezo za Allah, ndi kupha kwawo aneneri popanda choonadi, ndi kunena kwawo kwakuti: “Mitima yathu yakutidwa (siingathe kuzindikira zomwe ukunena iwe Muhammad {s.a.w}).” (Ai, Siinakutidwe ndi chilichonse), koma Allah waidinda zidindo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo; tero sakhulupirira koma pang’ono pokha. info
التفاسير:

external-link copy
156 : 4

وَبِكُفۡرِهِمۡ وَقَوۡلِهِمۡ عَلَىٰ مَرۡيَمَ بُهۡتَٰنًا عَظِيمٗا

Chifukwanso cha kusakhulupirira kwawo ndi kumnamizira kwawo Mariya bodza lalikulu (kuti wabala Isa (Yesu) m’njira ya chiwerewere); info
التفاسير:

external-link copy
157 : 4

وَقَوۡلِهِمۡ إِنَّا قَتَلۡنَا ٱلۡمَسِيحَ عِيسَى ٱبۡنَ مَرۡيَمَ رَسُولَ ٱللَّهِ وَمَا قَتَلُوهُ وَمَا صَلَبُوهُ وَلَٰكِن شُبِّهَ لَهُمۡۚ وَإِنَّ ٱلَّذِينَ ٱخۡتَلَفُواْ فِيهِ لَفِي شَكّٖ مِّنۡهُۚ مَا لَهُم بِهِۦ مِنۡ عِلۡمٍ إِلَّا ٱتِّبَاعَ ٱلظَّنِّۚ وَمَا قَتَلُوهُ يَقِينَۢا

Ndikuyankhula kwawo (kwakuti): “Ife tamupha Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, Mtumiki wa Allah; pomwe sadamuphe ndipo sadampachike pa mtanda. Koma adasokonezedwa (ndi munthu wina namuganizira kuti ndi Isa (Yesu). Ndithudi, amene akutsutsana pankhaniyi (Ayuda ndi Akhrisitu) ali m’chikaiko pa iyo; alibe kudziwa kotsimikizika, koma akungotsatira zongoganizira. Ndipo, sadamuphe mosimikiza (kuti ndi iye). info
التفاسير:

external-link copy
158 : 4

بَل رَّفَعَهُ ٱللَّهُ إِلَيۡهِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمٗا

Koma Allah adamkweza kwa Iye ndipo Allah Ndimwini mphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
159 : 4

وَإِن مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ إِلَّا لَيُؤۡمِنَنَّ بِهِۦ قَبۡلَ مَوۡتِهِۦۖ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يَكُونُ عَلَيۡهِمۡ شَهِيدٗا

Palibe aliyense mwa anthu omwe adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) koma kuti azamkhulupirira iye (Yesu kuti sadali mulungu) imfa yake (Yesuyo) isadadze (izi zizachitika pamene Yesuyo azabwerenso padziko lapansi kumapeto kwa dziko). Nayenso (Yesu) pa siku la chiweruziro adzaikira umboni pa iwo (kuti iye adali chabe kapolo wa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
160 : 4

فَبِظُلۡمٖ مِّنَ ٱلَّذِينَ هَادُواْ حَرَّمۡنَا عَلَيۡهِمۡ طَيِّبَٰتٍ أُحِلَّتۡ لَهُمۡ وَبِصَدِّهِمۡ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ كَثِيرٗا

Chifukwa chakuchita kwawo zoipa, awo Ayuda, tidaletsa kwa iwo zinthu zabwino (zakudya) zomwe zidali zovomerezeka kwa iwo; ndiponso chifukwa cha kutsekereza kwawo anthu ambiri kuyenda panjira ya Allah. info
التفاسير:

external-link copy
161 : 4

وَأَخۡذِهِمُ ٱلرِّبَوٰاْ وَقَدۡ نُهُواْ عَنۡهُ وَأَكۡلِهِمۡ أَمۡوَٰلَ ٱلنَّاسِ بِٱلۡبَٰطِلِۚ وَأَعۡتَدۡنَا لِلۡكَٰفِرِينَ مِنۡهُمۡ عَذَابًا أَلِيمٗا

Ndi kudya kwawo riba (katapira) pomwe adaletsedwa kuti asadye; ndiponso chifukwa chakudya kwawo chuma cha anthu mwachinyengo. Ndipo osakhulupirira mwa iwo tawakonzera chilango chopweteka. info
التفاسير:

external-link copy
162 : 4

لَّٰكِنِ ٱلرَّٰسِخُونَ فِي ٱلۡعِلۡمِ مِنۡهُمۡ وَٱلۡمُؤۡمِنُونَ يُؤۡمِنُونَ بِمَآ أُنزِلَ إِلَيۡكَ وَمَآ أُنزِلَ مِن قَبۡلِكَۚ وَٱلۡمُقِيمِينَ ٱلصَّلَوٰةَۚ وَٱلۡمُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱلۡمُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ أُوْلَٰٓئِكَ سَنُؤۡتِيهِمۡ أَجۡرًا عَظِيمًا

Koma mwa iwo amene azama pa maphunziro, ndi okhulupirira (onsewo) akukhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zimene zidavumbulutsidwa patsogolo pako. Ndipo omwe akupitiriza kupemphera Swala, ndi kupereka Zakaati, ndi kukhulupirira Allah komanso tsiku lachimaliziro, iwo tidzawapatsa malipiro aakulu. info
التفاسير: