[110] Apa tsopano akufotokoza mmene chuma chamasiye angachigawire ponena kuti m’Chisilamu akazi akuwalola kuwagawirako chuma cha abale awo, osati kuti amuna okha ndiwo, owagawira. Koma gawo lomwe mkazi amapatsidwa limacheperapo poyerekeza ndi gawo lomwe mwamuna amalandira. Chifukwa chakuti mwamuna ndiye ali ndi udindo waukulu poyerekeza ndi mkazi. Mwamuna ali ndi udindo woyang’anira mkazi wake, ana ake ndi makolo ake. Koma mkazi alibe udindo woyang’anira mwamuna wake. Ndiponso alibe udindo woyang’anira mwana kapena makolo ake, pokhapokha ngati tate wa anawo ali wochepa nzeru. Zikatero mpomwe mkaziyo amakhala ndi udindo woyang’anira ana ake.
[111] Chuma nchinthu chimene chimachotsa moyo wa munthu mmalomwake, makamaka ngati chikupezeka m’njira yaulere yosachivutikira, monga chilili chuma chamasiye. Choncho amene alibepo gawo pa chumacho amangoti diso tong’o, kusilira. Ndipo nchifukwa chake Allah apa akunena kuti pogawa chuma chamasiyecho ngati achibale atabwerapo omwe alibepo gawo pa chumacho, awapatseko kachinthu kochepa ndi kuwapepesa kuti chomwe awapatsacho nchochepa.
[112] Apa akufotokoza za kagawidwe ka chuma chamasiye (mirath).
a) Ngati munthu wamwalira nkusiya ana amuna ndi akazi tero mwana wamwamuna adzapeza magawo awiri ndipo wamkazi adzapeza gawo limodzi.
b) Munthu akafa nkusiya ana akazi okha, awiri kapena ochulukirapo, anawo adzatenga magawo awiri achumacho. Ndipo onsewo alandire mofanana. Pasapezeke wotenga zochuluka kuposa wina.
Tsono gawo lomwe latsala lidzaperekedwa kwa ena oti awagawire ngati alipo. Ngati palibe, ndiye kuti gawolo lidzaperekedwanso kwa ana akaziwo.
N.B Magawo awiri m’magawo atatu (2/3), apa akutanthauza kuti chuma chonsecho amachigawa m’magawo atatu ofanana. Ndipo akaziwo nkulandira magawo awiri mwa magawo atatuwo.
c) Ngati munthu atamwalira nkusiya mwana mmodzi wamkazi, ndiye kuti chumacho achigawe magawo awiri ofanana. Gawo limodzi mwa magawo awiri aja alipereke kwa mwana wamkaziyo. Ndipo gawo lotsalalo alipereke kwa ena ofunika kuwagawira ngati alipo. Ngati palibe, aliperekenso kwa mwana yemweyo. Lamulo la adzukulu likufanana ndi lamulo la ana ngati wakufayo adalibe ana koma adzukulu ake okha.
d) Munthu akafa nkusiya ana ndi makolo ake, (tate ndi mayi), tero tate adzapeza gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi (1/6) a chumacho. Nayenso mayi adzapeza gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi (1/6). Ndipo chuma chotsalacho adzalandira ndi ana kapena adzukulu a muntnu wakufayo.
e) Munthu akafa nkusiya tate wake ndi mayi wake basi, popanda ana ndi adzukulu choncho apa mayi adzalandira gawo limodzi mwa magawo atatu a chumacho. Ndipo tate adzatenga magawo awiri.
f) Munthu akafa nkusiya mayi wake yekha ndi abale ake obadwa nawo kwa mayi ndi bambo mmodzi, kapena akumbali ya kwabambo okha kapena akumbali yamayi okha, apa mayi adzalandira gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi a chumacho. Anthu oyenera kuwagawira chuma chamasiye asawagawire msanga chumacho mpaka ngongole zonse za wakufayo atazibweza. Ndiponso mpaka apereke chilawo (wasiya) chomwe wakufayo adanena kuti chidzachitike. Owagawira chumawo asakhale anthu osusuka ndi chumacho. choyamba aonetsetse kuti izi zonse zakwaniritsidwa. Komatu chilawocho chisapyole pagawo limodzi mwamagawo atatu (1/3) achumacho. Chikapyolera pamenepa ndiye kuti choonjezerapocho sichivomerezedwa.