ශුද්ධවූ අල් කුර්ආන් අර්ථ කථනය - චිචේවා පරිවර්තනය - කාලිද් ඉබ්රාහීම් බීතාලා

පිටු අංක:close

external-link copy
60 : 4

أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ يَزۡعُمُونَ أَنَّهُمۡ ءَامَنُواْ بِمَآ أُنزِلَ إِلَيۡكَ وَمَآ أُنزِلَ مِن قَبۡلِكَ يُرِيدُونَ أَن يَتَحَاكَمُوٓاْ إِلَى ٱلطَّٰغُوتِ وَقَدۡ أُمِرُوٓاْ أَن يَكۡفُرُواْ بِهِۦۖ وَيُرِيدُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَن يُضِلَّهُمۡ ضَلَٰلَۢا بَعِيدٗا

Kodi sukuwaona omwe akungonena chabe kuti akhulupirira zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zomwe zidavumbulutsidwa patsogolo pako, pomwe iwo akufuna kuti akaweruzidwe ndi maweruzo osagwirizana ndi Shariya, pomwenso alamulidwa kukana njira zotere? Koma satana akufuna kuwasokeretsa, kusokera kwakutali. info
التفاسير:

external-link copy
61 : 4

وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ تَعَالَوۡاْ إِلَىٰ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ وَإِلَى ٱلرَّسُولِ رَأَيۡتَ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ يَصُدُّونَ عَنكَ صُدُودٗا

Ndipo akauzidwa: “Idzani ku zomwe Allah wavumbulutsa, ndiponso (idzani) kwa Mtumiki.” Uwaona achinyengo akudziika kutali kwabasi ndi iwe. info
التفاسير:

external-link copy
62 : 4

فَكَيۡفَ إِذَآ أَصَٰبَتۡهُم مُّصِيبَةُۢ بِمَا قَدَّمَتۡ أَيۡدِيهِمۡ ثُمَّ جَآءُوكَ يَحۡلِفُونَ بِٱللَّهِ إِنۡ أَرَدۡنَآ إِلَّآ إِحۡسَٰنٗا وَتَوۡفِيقًا

Kodi zingakhale bwanji litawabwerera vuto chifukwa cha zomwe manja awo adatsogoza? Kenako nkukudzera (iwe Mtumiki) uku akulumbira: “Tikulumbira Allah; sitinafune china chilichonse koma zabwino zokha ndi chimvano.” info
التفاسير:

external-link copy
63 : 4

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ يَعۡلَمُ ٱللَّهُ مَا فِي قُلُوبِهِمۡ فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ وَعِظۡهُمۡ وَقُل لَّهُمۡ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ قَوۡلَۢا بَلِيغٗا

Iwo ndi omwe Allah akudziwa zomwe zili m’mitima mwawo. Choncho dzipatule kwa iwo, ndipo alangize ndi kuwauza mawu ogwira mtima. info
التفاسير:

external-link copy
64 : 4

وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن رَّسُولٍ إِلَّا لِيُطَاعَ بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ وَلَوۡ أَنَّهُمۡ إِذ ظَّلَمُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ جَآءُوكَ فَٱسۡتَغۡفَرُواْ ٱللَّهَ وَٱسۡتَغۡفَرَ لَهُمُ ٱلرَّسُولُ لَوَجَدُواْ ٱللَّهَ تَوَّابٗا رَّحِيمٗا

Ndipo sitidamtumize mtumiki aliyense koma kuti azimveredwa mwa lamulo la Allah. Ngati akadakudzera pamene adadzichitira okha zoipa, (chifukwa chokafuna chiweruzo cha satana) napempha chikhululuko kwa Allah (naye) Mtumiki nkuwapempheranso chikhululuko, ndithudi, akadampeza Allah ali Wolandira kulapa kwawo ali Wachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
65 : 4

فَلَا وَرَبِّكَ لَا يُؤۡمِنُونَ حَتَّىٰ يُحَكِّمُوكَ فِيمَا شَجَرَ بَيۡنَهُمۡ ثُمَّ لَا يَجِدُواْ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ حَرَجٗا مِّمَّا قَضَيۡتَ وَيُسَلِّمُواْ تَسۡلِيمٗا

Ndikulumbira (m’choonadi cha) Mbuye wako, iwo sangakhale okhulupirira moona pokhapokha akuyese muweruzi wawo pa zomwe akukangana pakati pawo. Kenako asaone vuto m’mitima yawo pa zomwe waweruza, ndipo adzipereke kwathunthu (pogonjera chiweruzo chako).[132] info

[132] Ngati anthu atakangana pachinthu ena nati chimenechi nchofunika pomwe ena akuti nchosafunika, onsewo abwere nkuyang’ana kuti mawu a Allah ndi mawu a Mtumiki akunena chiyani pachinthu choterecho. Tsono akapeza malangizo a Allah ndi Mtumiki pachimenecho awatsatire. Aliyense wa iwo asakhumudwe poona kuti zomwe amalimbikira sindizo zomwe Mtumiki (s.a.w) adaphunzitsa. Koma agonjere kwathunthu kuzophunzitsa za Mtumikizo. Chilichonse chimene Mtumiki walangiza asawiringule nacho. Koma angotsatira basi.

التفاسير: