[148] Iblis pamene adampirikitsa kumwamba iye adauza Allah kuti akazikometsera zolengedwa zake machimo. Allah adamuuza kuti sangathe kuzisokereza mwamphamvu, mozikakamiza, zifune zisafune. Aliyense amene akamtsata ndiye kuti akamtsata mwachifuniro chake. Sikuti mogonjetsedwa ndi mphamvu za satana kotero kuti iye sangathe kulimbana naye iyayi. Satana alibe mphamvu zokakamizira anthu.
[149] (1) Kukhala ndi chiyembekezo choti Allah adzawakhululukira pakuti iye ngokhululuka, Ngwachifundo. (2) Kuti ukachita zakutizakuti kapena ukawerenga duwa yakutiyakuti machimo ako onse adzakufafanizira ngakhale kuti udakwatula zinthu za anthu. (3) Kuti wolemekezeka uje adzatiwombola ngati tilumikizana naye. (4) Kuti mneneri wakutiwakuti adzaitana omtsatira ake kuti akalowe ku Munda wa mtendere. (5) Kuti Mtumiki sadzakhala wokondwa kuona anthu ake akuponyedwa ku Moto. (6) Kukhala ndi chiyembekezo choti ngati munthu ndiwe Msilamu basi sukalowa ku Jahannam. Ndipo satanayu amanyenganso Akhrisitu kuti ngati akhulupilira Isa (Yesu) basi sakalowa ku Moto. Ndipo Ayuda amawauzanso chimodzimodzi kuti ngati akhulupilira m’chipembedzo cha chiyuda sakalowa ku Moto. Nawonso opembedza moto ndi Abudha amawauzanso chimodzimodzi kuti ngati atsata chibudha basi apulumuka.