[139] Swala yopemphera pagulu (jamaa) akuilimbikitsa zedi ngakhale kuti anthu ali pakati pa nkhondo. Ngati nthawi ya Swala yakwana akuwauza kuti apemphere pagulu, koma asapemphere onse nthawi imodzi. Anthuwo agawike m’magulu awiri. Gulu lina liyang’ane komwe kuli adani, ndipo gulu lina likhale likupemphera pamodzi ndi (Imamu) mtsogoleri wawo. Komatu Swala akunkhondo amaswali raka ziwiriziwiri (Swala iliyonse) kupatula Swala ya Magharibi. Tsono Imamu adzapemphera raka imodzi ndi awo omwe akupemphera nawo. Akaimilira kuti apemphere raka yachiwiri, aja omwe anali kupemphera naye aimilire ndi kupemphera raka yotsalayo mwachangu atamsiya imamu ali chiimilire. Ndipo apite kukalowa m’malo mwa anzawo omwe anali kuyang’ana komwe kuli adani. Tsono anzawowo adze nkudzapemphera ndi Imamu. Imamu akamaliza raka yake yachiwiri, iwo aimilire nkumaliza raka yawo yachiwiri. Komatu popempherapo zida zawo zikhale atazikoleka m’matupi mwawo pokhapokha ngati pali zifukwa zoikitsa zidazo pansi, zomwe azitchula kumapeto a ndimeyo
[140] Nkofunika nthawi zonse Msilamu kukumbukira Allah.osati panthawi yokha yopemphera koma amkumbukire m’chikhalidwe chake chonse ndi m’zochita zake zonse. Nthawi zonse apewe zomwe Allah waletsa ndi kutsata malamulo ake.
[141] Apa akuwalamula Asilamu kuti amenyere chipembedzo chawo ngakhale atapeza mavuto amtundumtundu. Chifukwa chomwe akupezera mavutowo nchachikulu zedi kuposa mavutowo palibe chinthu chachikulu chimene munthu angachipeze chabe popanda kuvutikira.