Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

Número de página:close

external-link copy
55 : 36

إِنَّ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ ٱلۡيَوۡمَ فِي شُغُلٖ فَٰكِهُونَ

Ndithu anthu aku Jannah (Munda wamtendere) lero akhala wotanganidwa ndi chisangalalo. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 36

هُمۡ وَأَزۡوَٰجُهُمۡ فِي ظِلَٰلٍ عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ مُتَّكِـُٔونَ

Iwo ndi akazi awo ali m’mithunzi uku atatsamira mipando (ya mtengo wapamwamba). info
التفاسير:

external-link copy
57 : 36

لَهُمۡ فِيهَا فَٰكِهَةٞ وَلَهُم مَّا يَدَّعُونَ

M’menemo apeza (mtundu uliwonse) wa zipatso ndiponso apeza chilichonse chimene akuchifuna. info
التفاسير:

external-link copy
58 : 36

سَلَٰمٞ قَوۡلٗا مِّن رَّبّٖ رَّحِيمٖ

“Mtendere (pa iwo)!” Limeneli ndi liwu lochokera kwa Mbuye (wawo), Wachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 36

وَٱمۡتَٰزُواْ ٱلۡيَوۡمَ أَيُّهَا ٱلۡمُجۡرِمُونَ

Ndipo dzipatuleni lero, inu oipa! info
التفاسير:

external-link copy
60 : 36

۞ أَلَمۡ أَعۡهَدۡ إِلَيۡكُمۡ يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ أَن لَّا تَعۡبُدُواْ ٱلشَّيۡطَٰنَۖ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوّٞ مُّبِينٞ

Kodi sindidakulangizeni, E inu ana a Adam kuti musapembedze satana? Ndithu, iye ndi mdani woonekera kwa inu? info
التفاسير:

external-link copy
61 : 36

وَأَنِ ٱعۡبُدُونِيۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ

Ndikuti ndipembedzeni Ine? Imeneyi ndi njira yolunjika. info
التفاسير:

external-link copy
62 : 36

وَلَقَدۡ أَضَلَّ مِنكُمۡ جِبِلّٗا كَثِيرًاۖ أَفَلَمۡ تَكُونُواْ تَعۡقِلُونَ

Ndithu (satana) adasokeretsa anthu ambiri mwa inu. Kodi simumaganizira mwanzeru? info
التفاسير:

external-link copy
63 : 36

هَٰذِهِۦ جَهَنَّمُ ٱلَّتِي كُنتُمۡ تُوعَدُونَ

Iyi ndi Jahena yomwe mumalonjezedwa. info
التفاسير:

external-link copy
64 : 36

ٱصۡلَوۡهَا ٱلۡيَوۡمَ بِمَا كُنتُمۡ تَكۡفُرُونَ

Iloweni lero, chifukwa cha kunkana kwanu (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
65 : 36

ٱلۡيَوۡمَ نَخۡتِمُ عَلَىٰٓ أَفۡوَٰهِهِمۡ وَتُكَلِّمُنَآ أَيۡدِيهِمۡ وَتَشۡهَدُ أَرۡجُلُهُم بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ

Lero titseka kukamwa kwawo. Ndipo manja awo atiyankhula ndipo miyendo yawo ichitira umboni pa zomwe amachita. info
التفاسير:

external-link copy
66 : 36

وَلَوۡ نَشَآءُ لَطَمَسۡنَا عَلَىٰٓ أَعۡيُنِهِمۡ فَٱسۡتَبَقُواْ ٱلصِّرَٰطَ فَأَنَّىٰ يُبۡصِرُونَ

Ndipo tikadafuna, tikadafafaniza maso awo; ndipo akadakhala akuthamangira njira; koma akadapenya chotani? info
التفاسير:

external-link copy
67 : 36

وَلَوۡ نَشَآءُ لَمَسَخۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ مَكَانَتِهِمۡ فَمَا ٱسۡتَطَٰعُواْ مُضِيّٗا وَلَا يَرۡجِعُونَ

Ndipo tikadafuna, tikadawasintha kukhala ndi maonekedwe a nyama pamalo pawo pomwepo (pamene adali), kotero kuti sakadatha kuyenda (kunka patsogolo) ngakhale kubwerera pambuyo. info
التفاسير:

external-link copy
68 : 36

وَمَن نُّعَمِّرۡهُ نُنَكِّسۡهُ فِي ٱلۡخَلۡقِۚ أَفَلَا يَعۡقِلُونَ

Ndipo amene tikumtalikitsira moyo wake, timam’bwezeranso pambuyo m’kalengedwe kake (ndi kukhala ngati mwana). Kodi bwanji saganizira mwanzeru? info
التفاسير:

external-link copy
69 : 36

وَمَا عَلَّمۡنَٰهُ ٱلشِّعۡرَ وَمَا يَنۢبَغِي لَهُۥٓۚ إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرٞ وَقُرۡءَانٞ مُّبِينٞ

Ndipo sitidamphunzitse (Mtumiki {s.a.w}) ndakatulo, ndipo nkosayenera kwa iye (kukhala mlakatuli). Qur’an sichina, koma ndichikumbutso ndi buku lomwe likulongosola chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
70 : 36

لِّيُنذِرَ مَن كَانَ حَيّٗا وَيَحِقَّ ٱلۡقَوۡلُ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ

Kuti liwachenjeze amene ali moyo, ndi kuti litsimikizike liwu (la chilango) pa osakhulupirira. info
التفاسير: