Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

Número de página:close

external-link copy
13 : 36

وَٱضۡرِبۡ لَهُم مَّثَلًا أَصۡحَٰبَ ٱلۡقَرۡيَةِ إِذۡ جَآءَهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ

Ndipo pereka kwa iwo (iwe Mneneri) fanizo la (nkhani ya) eni mudzi pamene atumiki (a Allah) adaudzera mudziwo (kuti akaaongole eni mudziwo). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 36

إِذۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهِمُ ٱثۡنَيۡنِ فَكَذَّبُوهُمَا فَعَزَّزۡنَا بِثَالِثٖ فَقَالُوٓاْ إِنَّآ إِلَيۡكُم مُّرۡسَلُونَ

Pamene tidatumiza atumiki awiri kwa iwo adawatsutsa; ndipo tidawalimbitsa iwo (awiriwo) potumiza wachitatu. (Atumiki atatuwo) adati: “Ife tatumidwa kwa inu.” info
التفاسير:

external-link copy
15 : 36

قَالُواْ مَآ أَنتُمۡ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُنَا وَمَآ أَنزَلَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مِن شَيۡءٍ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا تَكۡذِبُونَ

(Eni mudzi) adati: “Inu ndi anthu ngati ife; (Allah) Wachifundo chambiri sadavumbulutse chilichonse (kwa munthu); inu simuli kanthu koma mukunena bodza.” info
التفاسير:

external-link copy
16 : 36

قَالُواْ رَبُّنَا يَعۡلَمُ إِنَّآ إِلَيۡكُمۡ لَمُرۡسَلُونَ

(Atumiki) adati: “Mbuye wathu (Amene watituma kwa inu) akudziwa kuti ife ndi otumidwadi kwa inu.” info
التفاسير:

external-link copy
17 : 36

وَمَا عَلَيۡنَآ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ

“Ndipo palibe china pa ife, koma kufikitsa mwachimvekere (uthenga wa Allah).” info
التفاسير:

external-link copy
18 : 36

قَالُوٓاْ إِنَّا تَطَيَّرۡنَا بِكُمۡۖ لَئِن لَّمۡ تَنتَهُواْ لَنَرۡجُمَنَّكُمۡ وَلَيَمَسَّنَّكُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٞ

(Eni mudzi) adati: “Ife tapeza tsoka chifukwa cha inu; ngati simusiya (ulaliki wanuwo wofuna kutichotsa ku chipembedzo chathu) tikugendani ndi miyala; ndipo kuchokera kwa ife chikukhudzani chilango chowawa.” info
التفاسير:

external-link copy
19 : 36

قَالُواْ طَٰٓئِرُكُم مَّعَكُمۡ أَئِن ذُكِّرۡتُمۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٞ مُّسۡرِفُونَ

(Atumiki) adati: “Tsoka lanu lili ndi inu (chifukwa cha kukana kwanu ndi kupitiriza kupembedza mafano). Kodi mukakumbutsidwa (ndi mawu omwe m’kati mwake muli mtendere wanu mukuti takudzetserani masoka; ndi kumatiopseza ndi chilango chowawa)? Koma inu ndi anthu olumpha malire.” info
التفاسير:

external-link copy
20 : 36

وَجَآءَ مِنۡ أَقۡصَا ٱلۡمَدِينَةِ رَجُلٞ يَسۡعَىٰ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱتَّبِعُواْ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Kenako munthu adadza akuthamanga kuchokera ku malekezero a mzindawo (ndipo) adati: “E inu anthu anga! Atsateni atumikiwa.” info
التفاسير:

external-link copy
21 : 36

ٱتَّبِعُواْ مَن لَّا يَسۡـَٔلُكُمۡ أَجۡرٗا وَهُم مُّهۡتَدُونَ

“Atsateni omwe sakupemphani malipiro (pa kukulangizani kwawo), ndipo iwo ngoongoka.” info
التفاسير:

external-link copy
22 : 36

وَمَالِيَ لَآ أَعۡبُدُ ٱلَّذِي فَطَرَنِي وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ

“Kodi nchiyani chingandiletse ine kupembedza Yemwe adandilenga? Ndipo kwa Iye ndi komwe inu nonse mudzabwerera.”. info
التفاسير:

external-link copy
23 : 36

ءَأَتَّخِذُ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةً إِن يُرِدۡنِ ٱلرَّحۡمَٰنُ بِضُرّٖ لَّا تُغۡنِ عَنِّي شَفَٰعَتُهُمۡ شَيۡـٔٗا وَلَا يُنقِذُونِ

“Kodi ndidzipangire milungu kusiya Iye (Allah)? Chipulumutso chawo sichingandipindulire chilichonse ngati (Allah) Wachifundo Chambiri atafuna kundichitira zoipa; ndipo siingandipulumutse.” info
التفاسير:

external-link copy
24 : 36

إِنِّيٓ إِذٗا لَّفِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٍ

“Ndithu ine ngati nditatero ndiye kuti ndili mchisokero choonekera poyera”. info
التفاسير:

external-link copy
25 : 36

إِنِّيٓ ءَامَنتُ بِرَبِّكُمۡ فَٱسۡمَعُونِ

“Ndithu ine ndakhulupirira Mbuye wanu choncho ndimvereni.” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 36

قِيلَ ٱدۡخُلِ ٱلۡجَنَّةَۖ قَالَ يَٰلَيۡتَ قَوۡمِي يَعۡلَمُونَ

Kudanenedwa (kwa iye): “Lowa m’Munda wamtendere.” Iye adati: “Ha! Anthu anga akadadziwa!” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 36

بِمَا غَفَرَ لِي رَبِّي وَجَعَلَنِي مِنَ ٱلۡمُكۡرَمِينَ

“Momwe Mbuye wanga wandikhululukira ndikundichita kukhala mmodzi wa opatsidwa ulemu (akadakhulupirira).” info
التفاسير: