Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

Número de página:close

external-link copy
41 : 36

وَءَايَةٞ لَّهُمۡ أَنَّا حَمَلۡنَا ذُرِّيَّتَهُمۡ فِي ٱلۡفُلۡكِ ٱلۡمَشۡحُونِ

Ndiponso pali chisonyezo kwa iwo (chosonyeza madalitso Athu pa iwo). Ndithu tidaukweza mtundu wawo mchombo chodzazidwa (ndi zonse zamoyo). info
التفاسير:

external-link copy
42 : 36

وَخَلَقۡنَا لَهُم مِّن مِّثۡلِهِۦ مَا يَرۡكَبُونَ

Ndipo tidawapangira chonga icho chomwe akuchikwera.[342] info

[342] Allah ndi Yemwe adapanga zombo ngakhale kuti zidapangidwa ndi manja a anthu, chifukwa Iye ndi Amene adaphunzitsa anthu kupanga zombozo.

التفاسير:

external-link copy
43 : 36

وَإِن نَّشَأۡ نُغۡرِقۡهُمۡ فَلَا صَرِيخَ لَهُمۡ وَلَا هُمۡ يُنقَذُونَ

Ndipo ngati titafuna tikhoza kuwamiza m’madzi, ndipo sangapezeke wowathandiza, ndiponso sangapulumutsidwe. info
التفاسير:

external-link copy
44 : 36

إِلَّا رَحۡمَةٗ مِّنَّا وَمَتَٰعًا إِلَىٰ حِينٖ

Koma (sitikuwamiza) chifukwa cha chifundo Chathu pa iwo ndi kuti asangalale kufikira nthawi yawo (yofera). info
التفاسير:

external-link copy
45 : 36

وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱتَّقُواْ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيكُمۡ وَمَا خَلۡفَكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ

Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Opani zomwe ziri patsogolo panu ndi zomwe ziri pambuyo panu kuti muchitiridwe chifundo.” (Iwo akunyoza malangizowo). info
التفاسير:

external-link copy
46 : 36

وَمَا تَأۡتِيهِم مِّنۡ ءَايَةٖ مِّنۡ ءَايَٰتِ رَبِّهِمۡ إِلَّا كَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ

Ndipo palibe chisonyezo chilichonse mwa zisonyezo za Mbuye wawo (zosonyeza umodzi Wake ndi kukhoza Kwake) chomwe chidawadzera popanda kuchinyoza (ndi kuchikana). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 36

وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ أَنفِقُواْ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُ قَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَنُطۡعِمُ مَن لَّوۡ يَشَآءُ ٱللَّهُ أَطۡعَمَهُۥٓ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ

Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Patsani (amphawi) zimene Allah wakupatsani.” Osakhulupirira amanena kwa okhulupirira: “Kodi tidyetse yemwe Allah akadafuna akadamdyetsa; (titsutsane ndi cholinga cha Allah)? Ndithu inu simuli kanthu koma muli m’kusokera koonekeratu.” info
التفاسير:

external-link copy
48 : 36

وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Ndipo akunena (mwachipongwe kwa okhulupirira): “Kodi lonjezo ili (lakudza kwa chiweruziro), lidzachitika liti, ngati mukunena zoona?” info
التفاسير:

external-link copy
49 : 36

مَا يَنظُرُونَ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ تَأۡخُذُهُمۡ وَهُمۡ يَخِصِّمُونَ

Palibe chimene akuyembekeza, koma ndi mkuwe umodzi womwe udzawamaliza mwadzidzidzi uku iwo akukangana. info
التفاسير:

external-link copy
50 : 36

فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ تَوۡصِيَةٗ وَلَآ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمۡ يَرۡجِعُونَ

Ndipo sangathe kuuza wina mawu pa chinthu, ndiponso sangathe kubwerera ku maanja awo. info
التفاسير:

external-link copy
51 : 36

وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَإِذَا هُم مِّنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ يَنسِلُونَ

Ndipo lipenga lidzaimbidwa (loukitsa akufa); iwo adzangozindikira akutuluka m’manda kunka kwa Mbuye wawo uku akuthamanga. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 36

قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَا مَنۢ بَعَثَنَا مِن مَّرۡقَدِنَاۜۗ هَٰذَا مَا وَعَدَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَصَدَقَ ٱلۡمُرۡسَلُونَ

Adzati: “Kalanga ife! Kodi ndani watidzutsa pogona pathu?” (Adzawauza): “Izi ndi zimene adalonjeza (Allah), Wachifundo chambiri ndi zimene adanena atumiki moona.” info
التفاسير:

external-link copy
53 : 36

إِن كَانَتۡ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ فَإِذَا هُمۡ جَمِيعٞ لَّدَيۡنَا مُحۡضَرُونَ

Sipadzakhala (china) koma mkuwe umodzi basi; adzangozindikira iwo onse atabweretsedwa patsogolo Pathu. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 36

فَٱلۡيَوۡمَ لَا تُظۡلَمُ نَفۡسٞ شَيۡـٔٗا وَلَا تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

“Ndipo mzimu uliwonse lero suponderezedwa pa chilichonse. Ndipo mulipidwa pa zokhazo munkachita.” info
التفاسير: