Vertaling van de betekenissen Edele Qur'an - Chichewa-vertaling - Khalid Ibrahim Beitala

Pagina nummer:close

external-link copy
15 : 12

فَلَمَّا ذَهَبُواْ بِهِۦ وَأَجۡمَعُوٓاْ أَن يَجۡعَلُوهُ فِي غَيَٰبَتِ ٱلۡجُبِّۚ وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡهِ لَتُنَبِّئَنَّهُم بِأَمۡرِهِمۡ هَٰذَا وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Ndipo pamene adanka naye ndi kugwirizana pakati pawo kuti amuike mchitsime chakuya, (adamuikadi). Ndipo tidamzindikiritsa iye (Yûsuf): “Ndithu udzawauza chinthu chawochi (chimene akuchitirachi) pomwe iwo sakudziwa.” info
التفاسير:

external-link copy
16 : 12

وَجَآءُوٓ أَبَاهُمۡ عِشَآءٗ يَبۡكُونَ

Ndipo adadza kwa bambo awo madzulo akulira, info
التفاسير:

external-link copy
17 : 12

قَالُواْ يَٰٓأَبَانَآ إِنَّا ذَهَبۡنَا نَسۡتَبِقُ وَتَرَكۡنَا يُوسُفَ عِندَ مَتَٰعِنَا فَأَكَلَهُ ٱلذِّئۡبُۖ وَمَآ أَنتَ بِمُؤۡمِنٖ لَّنَا وَلَوۡ كُنَّا صَٰدِقِينَ

Akunena: “E bambo wathu! Tidapita kokapikisana (kuthamanga), ndipo tidamsiya Yûsuf pomwe padali ziwiya zathu; choncho mimbulu yamudya koma inu simutikhulupirira (pa zimene tikukuuzanizi) ngakhale kuti tikunena zoona.” info
التفاسير:

external-link copy
18 : 12

وَجَآءُو عَلَىٰ قَمِيصِهِۦ بِدَمٖ كَذِبٖۚ قَالَ بَلۡ سَوَّلَتۡ لَكُمۡ أَنفُسُكُمۡ أَمۡرٗاۖ فَصَبۡرٞ جَمِيلٞۖ وَٱللَّهُ ٱلۡمُسۡتَعَانُ عَلَىٰ مَا تَصِفُونَ

Ndiponso adabwera ndi mkanjo wake (wa Yûsuf) uli ndi magazi abodza. (Bambo wawo pamene adauona mkanjowo uli wosang’ambika) adati: “Koma mitima yanu yakukometserani chinthu (chomwe mwamchitira mnzanu mwa chifuniro chanu; ndipo chimene ine ndingachite ndi) kupirira kwabwino; ndipo Allah ndi Wopemphedwa chithandizo pa zimene mukunenazi.” info
التفاسير:

external-link copy
19 : 12

وَجَآءَتۡ سَيَّارَةٞ فَأَرۡسَلُواْ وَارِدَهُمۡ فَأَدۡلَىٰ دَلۡوَهُۥۖ قَالَ يَٰبُشۡرَىٰ هَٰذَا غُلَٰمٞۚ وَأَسَرُّوهُ بِضَٰعَةٗۚ وَٱللَّهُ عَلِيمُۢ بِمَا يَعۡمَلُونَ

Ndipo aulendo adadza (pafupi ndi chitsimecho) ndipo adatuma wotunga madzi wawo, choncho iye adaponya ndowa yake (m’chitsime, ndipo akukoka ndowa ija adaona mwana) nati: “Eee, chisangalalo changa! Aka kamwana kakamuna!” Pomwepo iwo (amene adalipo pa chitsimepo) adam’bisa (kwa a paulendo anzawo) monga katundu wamalonda (yemwe adamgula). Koma Allah ankadziwa zimene adali kuchita (ndipo adanka naye ku Iguputo).[230] info

[230] 19-20. Apa tikuona kuti kugulitsana anthu kudayambika kalekale zedi kuyambira zaka 4,000 zapitazo mu nthawi ya umbuli. Koma adani achipembedzo cha Chisilamu akuchinamizira Chisilamu kuti ndicho chidadza ndi ukapolo wogulitsa anthu. Chikhalirecho Chisilamu ndicho chidadza kuzalimbikitsa zopereka ufulu kwa kapolo.

التفاسير:

external-link copy
20 : 12

وَشَرَوۡهُ بِثَمَنِۭ بَخۡسٖ دَرَٰهِمَ مَعۡدُودَةٖ وَكَانُواْ فِيهِ مِنَ ٱلزَّٰهِدِينَ

Ndipo adamgulitsa pa mtengo wochepa ndi ndalama zapang’ono, zowerengeka (poopa kuti angawadzere eni mwanayo). Ndipo sadalabadire za iye. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 12

وَقَالَ ٱلَّذِي ٱشۡتَرَىٰهُ مِن مِّصۡرَ لِٱمۡرَأَتِهِۦٓ أَكۡرِمِي مَثۡوَىٰهُ عَسَىٰٓ أَن يَنفَعَنَآ أَوۡ نَتَّخِذَهُۥ وَلَدٗاۚ وَكَذَٰلِكَ مَكَّنَّا لِيُوسُفَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلِنُعَلِّمَهُۥ مِن تَأۡوِيلِ ٱلۡأَحَادِيثِۚ وَٱللَّهُ غَالِبٌ عَلَىٰٓ أَمۡرِهِۦ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ

Ndipo uja (amene) adamgula ku Iguputo, adati kwa mkazi wake: “Mkonzere pokhala pabwino (kapolo uyu), mwina angatithandize kapena tingamsandutse kukhala mwana (wathu).” Motero tidamkhazika Yûsuf m’dziko (la Iguputo mwachisangalalo), ndi kuti timphunzitse kumasulira nkhani (maloto). Ndipo Allah Ngopambana pa zinthu Zake (zimene wafuna kuti zichitike); koma anthu ambiri sadziwa. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 12

وَلَمَّا بَلَغَ أَشُدَّهُۥٓ ءَاتَيۡنَٰهُ حُكۡمٗا وَعِلۡمٗاۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo pamene (Yûsuf) adafika pa nsinkhu wozindikira zinthu, tidampatsa kuweruza ndi nzeru. Umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino. info
التفاسير: