Vertaling van de betekenissen Edele Qur'an - Chichewa-vertaling - Khalid Ibrahim Beitala

Yûsuf

external-link copy
1 : 12

الٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ

Alif-Lâm-Ra. Izi ndi Ayah (ndime) za m’buku lomwe likuonetsera poyera (chilichonse chofunika). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 12

إِنَّآ أَنزَلۡنَٰهُ قُرۡءَٰنًا عَرَبِيّٗا لَّعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ

Ndithu Ife taivumbulutsa Qur’an ya Charabu kuti inu muzindikire. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 12

نَحۡنُ نَقُصُّ عَلَيۡكَ أَحۡسَنَ ٱلۡقَصَصِ بِمَآ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ وَإِن كُنتَ مِن قَبۡلِهِۦ لَمِنَ ٱلۡغَٰفِلِينَ

Ife tikukusimbira nkhani zabwino zedi pokuzindikiritsa Qur’an iyi; ndithu udali mmodzi mwa osadziwa zinthu, isanakufike. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 12

إِذۡ قَالَ يُوسُفُ لِأَبِيهِ يَٰٓأَبَتِ إِنِّي رَأَيۡتُ أَحَدَ عَشَرَ كَوۡكَبٗا وَٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ رَأَيۡتُهُمۡ لِي سَٰجِدِينَ

Akumbutse za Yûsuf pamene adauza bambo wake: “E inu bambo wanga! Ndithu ine ndaona kutulo nyenyezi khumi ndi imodzi, dzuwa ndi mwezi, zonsezo ndaziona zikundigwadira.” info
التفاسير: