[133] Pamene Mtumiki (s.a.w) adasamuka ku Makka kukakhala ku Madina, Asilamu ena aamuna ndi aakazi adatsalira ku Makka chifukwa chakuti abale awo adawaletsa. Ndipo chifukwa chakufooka kwawo sadathe kuthawa mozemba namangokhala konko ku Makka akuwachitira zoipa zambiri ndi kumawanyoza. Choncho Asilamu adawauza kuti ngati kuzakhale kololezedwa kuchita nawo nkhondo Aquraish a m’Makka adzamenyane nawo Aquraishwo molimba kufikira adzawapulumutse. Asilamu adakwaniritsa lonjezolo. Adamenya nkhondo mpaka kugonjetsa mzinda wa Makka ndi kuwapulumutsa anzawo amene adali kupempha Allah kwa nthawi yaitali kuti awapulumutse ku anthu oipa.