[184] Chifundo cha Allah chimawafika anthu omwe amachitiranso chifundo anzawo. Ndipo amene sachitira anzawo chifundo sangapezenso chifundo cha Allah. Choncho tiyeni tilimbikire kuthandiza ofooka ndi osowa chithandizo. Ngati sititero ndiye kuti chifundo cha Allah chidzakhala kutali nafe.
[185] Mmene Allah amaiukitsira nthaka youma ndi madzi amvula, nameretsa mmera wosiyanasiyana, momwemonso ndimo adzawaukitsira akufa. Palibe chimene chingamkanike.