Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Khalid Ibrahim Betyala

Numero di pagina: 161:151 close

external-link copy
88 : 7

۞ قَالَ ٱلۡمَلَأُ ٱلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ لَنُخۡرِجَنَّكَ يَٰشُعَيۡبُ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَكَ مِن قَرۡيَتِنَآ أَوۡ لَتَعُودُنَّ فِي مِلَّتِنَاۚ قَالَ أَوَلَوۡ كُنَّا كَٰرِهِينَ

۞ Akuluakulu omwe adadzikuza mwa anthu ake, adanena: “Tikupirikitsa, iwe Shuaib m’mudzi mwathu muno ndi amene akhulupirira pamodzi nawe, pokhapokha mutabwerera ku chipembedzo chathu.” (Iye) adati: “Kodi ngakhale kuti tikuchida?” info
التفاسير:

external-link copy
89 : 7

قَدِ ٱفۡتَرَيۡنَا عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا إِنۡ عُدۡنَا فِي مِلَّتِكُم بَعۡدَ إِذۡ نَجَّىٰنَا ٱللَّهُ مِنۡهَاۚ وَمَا يَكُونُ لَنَآ أَن نَّعُودَ فِيهَآ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُ رَبُّنَاۚ وَسِعَ رَبُّنَا كُلَّ شَيۡءٍ عِلۡمًاۚ عَلَى ٱللَّهِ تَوَكَّلۡنَاۚ رَبَّنَا ٱفۡتَحۡ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَ قَوۡمِنَا بِٱلۡحَقِّ وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلۡفَٰتِحِينَ

“Ngati titabwerera m’chipembedzo chanu pambuyo potipulumutsa Allah m’menemo, ndiye kuti tampekera Allah bodza. Sikungatheke kwa ife kubwerera m’chipembedzo chimenecho pokhapokha atafuna Allah, Mbuye wathu. Mbuye wathu Ngodziwa zonse. Ndipo kwa Allah Yekha ndiko tayadzamira. Mbuye wathu! Weruzani mwa choonadi pakati pathu ndi pakati pa anthu athu. Inu Ngabwino poweruza kuposa oweruza.” info
التفاسير:

external-link copy
90 : 7

وَقَالَ ٱلۡمَلَأُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ لَئِنِ ٱتَّبَعۡتُمۡ شُعَيۡبًا إِنَّكُمۡ إِذٗا لَّخَٰسِرُونَ

Ndipo akuluakulu mwa anthu ake omwe sadakhulupirire adati: “Ngati mutsatira Shuaib ndithudi pamenepo ndiye kuti mukhala otayika.” info
التفاسير:

external-link copy
91 : 7

فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلرَّجۡفَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دَارِهِمۡ جَٰثِمِينَ

Choncho chivomerezi chidawaononga mwadzidzidzi motero adapezeka akufa chigwadire mnyumba zawo. info
التفاسير:

external-link copy
92 : 7

ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ شُعَيۡبٗا كَأَن لَّمۡ يَغۡنَوۡاْ فِيهَاۚ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ شُعَيۡبٗا كَانُواْ هُمُ ٱلۡخَٰسِرِينَ

Amene adamutsutsa Shuaib adakhala ngati sadakhalepo m’mudzimo. Amene adamutsutsa Shuaib ndi omwe adali otayika. info
التفاسير:

external-link copy
93 : 7

فَتَوَلَّىٰ عَنۡهُمۡ وَقَالَ يَٰقَوۡمِ لَقَدۡ أَبۡلَغۡتُكُمۡ رِسَٰلَٰتِ رَبِّي وَنَصَحۡتُ لَكُمۡۖ فَكَيۡفَ ءَاسَىٰ عَلَىٰ قَوۡمٖ كَٰفِرِينَ

(Pamene nthawi yakuonongeka kwawo idayandikira, Shuaib adatuluka m’mudzimo pamodzi ndi aja adakhulupirira) nawasiya oipawo (kunka kutali) uku akunena: “E inu anthu anga! Ndinafikitsadi uthenga wa Mbuye wanga ndipo ndinakuchenjezani ndiye nchotani ndidandaule za anthu okanira.” info
التفاسير:

external-link copy
94 : 7

وَمَآ أَرۡسَلۡنَا فِي قَرۡيَةٖ مِّن نَّبِيٍّ إِلَّآ أَخَذۡنَآ أَهۡلَهَا بِٱلۡبَأۡسَآءِ وَٱلضَّرَّآءِ لَعَلَّهُمۡ يَضَّرَّعُونَ

Ndipo palibe pamene tidamtuma mneneri aliyense m’mudzi uliwonse (nkumukana) koma tinkawalanga eni mudziwo ndi masautso ndi mavuto kuti afatse (ndi kulambira Allah; koma ayi adakanika). info
التفاسير:

external-link copy
95 : 7

ثُمَّ بَدَّلۡنَا مَكَانَ ٱلسَّيِّئَةِ ٱلۡحَسَنَةَ حَتَّىٰ عَفَواْ وَّقَالُواْ قَدۡ مَسَّ ءَابَآءَنَا ٱلضَّرَّآءُ وَٱلسَّرَّآءُ فَأَخَذۡنَٰهُم بَغۡتَةٗ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Kenako tinasintha pamalo pa choipa pobweretsapo chabwino, (tidawachotsera masautso ndi mavuto ngakhale sadali okhulupirira) mpaka anachuluka, ndi kuchulukanso chuma chawo; anayamba kunena kuti: “Masautso ndi mavuto adawakhudzaponso makolo athu. (Zoterezi sizachilendo kwa ife).” Choncho tidawaononga mwadzidzidzi asakudziwa. info
التفاسير: