[180] Allah akutiuza kuti tivale nsalu zomwe Allah adatipangira kuti zikongoletse matupi athu. Komatu akutilamulanso kuti tivale nsalu zokongoletsa mitima yathu; nsalu yomwe njotsatira nayo malamulo a Allah ndi kusiya zomwe Iye waletsa; ndi kuchita zokhazo zomwe Allah walamula. Nsalu imeneyi ndi “takuwa” (kuopa Allah). Sibwino kukongoletsa kunja kwa thupi kokha pomwe mu mtima mwadzaza zauve.