Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala

Lambar shafi:close

external-link copy
149 : 3

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِن تُطِيعُواْ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يَرُدُّوكُمۡ عَلَىٰٓ أَعۡقَٰبِكُمۡ فَتَنقَلِبُواْ خَٰسِرِينَ

E inu amene mwakhulupirira! Ngati muwamvere amene sadakhulupirire, akubwezerani kumbuyo kwanu (kumachitidwe achikunja) tero mudzakhala otaika. info
التفاسير:

external-link copy
150 : 3

بَلِ ٱللَّهُ مَوۡلَىٰكُمۡۖ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلنَّٰصِرِينَ

Komatu Allah ndiye Mbuye wanu. Iye Ngwabwino kwabasi kuposa athandizi (ena onse). info
التفاسير:

external-link copy
151 : 3

سَنُلۡقِي فِي قُلُوبِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ ٱلرُّعۡبَ بِمَآ أَشۡرَكُواْ بِٱللَّهِ مَا لَمۡ يُنَزِّلۡ بِهِۦ سُلۡطَٰنٗاۖ وَمَأۡوَىٰهُمُ ٱلنَّارُۖ وَبِئۡسَ مَثۡوَى ٱلظَّٰلِمِينَ

Tiponya mantha m’mitima mwa amene sadakhulupirire chifukwa chakumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadatsitsire umboni (wosonyeza umulungu wawo) ndipo malo awo adzakhala ku Moto. Taonani kuipitsitsa malo a anthu ochita zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
152 : 3

وَلَقَدۡ صَدَقَكُمُ ٱللَّهُ وَعۡدَهُۥٓ إِذۡ تَحُسُّونَهُم بِإِذۡنِهِۦۖ حَتَّىٰٓ إِذَا فَشِلۡتُمۡ وَتَنَٰزَعۡتُمۡ فِي ٱلۡأَمۡرِ وَعَصَيۡتُم مِّنۢ بَعۡدِ مَآ أَرَىٰكُم مَّا تُحِبُّونَۚ مِنكُم مَّن يُرِيدُ ٱلدُّنۡيَا وَمِنكُم مَّن يُرِيدُ ٱلۡأٓخِرَةَۚ ثُمَّ صَرَفَكُمۡ عَنۡهُمۡ لِيَبۡتَلِيَكُمۡۖ وَلَقَدۡ عَفَا عَنكُمۡۗ وَٱللَّهُ ذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndithudi, Allah adakutsimikizirani lonjezo lake (lakuti muwagonjetsa adani). Choncho mudali kuwapha mwachilolezo Chake kufikira pamene mudafooka ndikuyamba kukangana za lamulolo, tero mudalinyozera pambuyo pokuonetsani zimene mumazikonda; (pamenepo mpomwe adasiya kukuthangatani). Alipo ena mwa inu amene akukonda dziko lapansi (zamdziko), ndipo alipo ena mwa inu amene akukonda tsiku lachimaliziro. Kenako (Allah) adakuchotsani pa iwo (adakusiitsani kuwamenya osakhulupirirawo) kuti akuyeseni mayeso. Koma Iye tsopano wakukhululukirani. Ndipo Allah ndi mwini kuchita zabwino pa okhulupirira.[94] info

[94] Apa akulongosola chifukwa chomwe Asilamu adapezera mavuto. Iwo adapeza mavuto chifukwa choswa lamulo la Mtumiki (s.a.w) lomwe adawalamula. Mtumiki (s.a.w) adaika pa phiri anthu makumi asanu (50) omwe adali akatswiri olasa mipaliro. Adawauza kuti asachokepo kuti ateteze gulu la Asilamu kuti adani asawamenye nkhondo powadzelera kumbuyo. Adanenetsa kwa iwo kuti asachoke pamalopo ngakhale ataona kuti anzawo akupambana kapena akugonja, kufikira Mtumiki atawalamula kuti achokepo. Koma ena mwa iwo adanyoza lamuloli pamene adaona kuti anzawo chammunsi mwa phirilo akupambana ndipo akuthamangitsa adani ndi kuwapha ndikumatola zotolatola za pankhondo. Choncho, iwo anatsika paphiripo nkusakanikirana ndi anzawo nayamba kutola nawo zotola zapankhondo. Mtsogoleri wawo adayesera umu ndi umu kuwaletsa koma sadamumvere kupatula ochepa okha amene adatsala pa phiripo. Pompo ngwazi zina za m’gulu la adani awowo zitaona kuti anthu omwe adali pa phiri achokapo, zidalitembenuza gulu lawo lankhondo nkuyamba kuwamenya Asilamu chakumbuyo. Potero ambiri adaphedwa ndi kuvulala.

التفاسير:

external-link copy
153 : 3

۞ إِذۡ تُصۡعِدُونَ وَلَا تَلۡوُۥنَ عَلَىٰٓ أَحَدٖ وَٱلرَّسُولُ يَدۡعُوكُمۡ فِيٓ أُخۡرَىٰكُمۡ فَأَثَٰبَكُمۡ غَمَّۢا بِغَمّٖ لِّكَيۡلَا تَحۡزَنُواْ عَلَىٰ مَا فَاتَكُمۡ وَلَا مَآ أَصَٰبَكُمۡۗ وَٱللَّهُ خَبِيرُۢ بِمَا تَعۡمَلُونَ

Kumbukirani pamene mudali kuthawa mwa liwiro popanda kumvera aliyense; pomwe Mtumiki adali kukuitanani, ali pambuyo panu. Ndipo (Allah) Adakupatsani madandaulo pa madandaulo. (Motero wakukhululukirani) kuti musadandaule pa zomwe zakudutsani, ngakhalenso (pa masautso) omwe akupezani. Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene muchita. info
التفاسير: