[90] Pamene Asilamu adamva ubwino waukulu umene angaupeze akafera pa nkhondoyo monga “Shahidi”, aliyense wa iwo adakhumba akadafera pa nkhondo yoteroyo, kuti akapeze ulemelerowo. Choncho Asilamu makumi asanu ndi awiri (70) adaphedwa pa nkhondo ya Uhudi mwa anthu mazana asanu ndi awiri (700) omwe adaima mwamphamvu kulimbana ndi anthu osakhulupilira omwe adalipo zikwi zitatu (3,000).
[91] Apa akunena mwatsatanetsatane kuti Mneneri Muhammad (s.a.w) ndi mtumiki basi yemwe ndimunthu monga alili anthu ena onse. Adafa monga momwe ena adafera. Koma ngakhale iye wafa anthu ena atsanzire chikhalidwe chake ndi zophunzitsa zake zomwe amaphunzitsa. Asabwelere m’mbuyo kusiya Chipembedzo poona kuti iye wafa.
[92] Apa akutilimbikitsa kuti tigwire ntchito yodzatipindulira pa tsiku lachiweruziro molimbika, tsiku lomwe ndilamoyo wosatha.
[93] Asilamu akuwauza kuti asataye mtima atawagonjetsa pa nkhondo iliyonse, kapena atawapeza masautso amtundu uliwonse. Chofunika nkupilira ndi kulimbana nawo mavutowo.