Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - Die Übersetzung in Chichewa - Khalid Ibrahim Bityala.

Al-Ma’idah

external-link copy
1 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَوۡفُواْ بِٱلۡعُقُودِۚ أُحِلَّتۡ لَكُم بَهِيمَةُ ٱلۡأَنۡعَٰمِ إِلَّا مَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡ غَيۡرَ مُحِلِّي ٱلصَّيۡدِ وَأَنتُمۡ حُرُمٌۗ إِنَّ ٱللَّهَ يَحۡكُمُ مَا يُرِيدُ

E inu amene mwakhulupirira! Kwaniritsani mapangano onse (omwe ali pakati panu ndi anthu anzanu). Kwalolezedwa kwa inu (kudya nyama ya) ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi), kupatula chomwe mukuuzidwa (kuti ncholetsedwa). Koma nkosaloledwa kwa inu kuchita ulenje mutalowa m’mapemphero a Hajj, (kapena muli m’nthaka yopatulika ya ku Makka). Ndithudi, Allah akulamula chimene wafuna.[155] info

[155] Chisilamu chimalemekeza zinthu zogwilira ntchito ya chipembedzo, monga ziweto zimene amazitumiza ku Makka ncholinga choti akazizinge kumeneko monga sadaka yopereka konko. Ndipo anthu okachita mapemphero a Hajjiwo, ziweto amaziveka zizindikiro zosonyeza kuti nziweto zomwe akukazipereka monga nsembe kwa Allah. Ndipo nyamazo zimakhala zopatulika. Choncho sibwino kuswa kupatulika kumeneku pozilanda mwachifwamba ndi kuzipha zisanafike pamalo pake poziphera.

التفاسير:

external-link copy
2 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تُحِلُّواْ شَعَٰٓئِرَ ٱللَّهِ وَلَا ٱلشَّهۡرَ ٱلۡحَرَامَ وَلَا ٱلۡهَدۡيَ وَلَا ٱلۡقَلَٰٓئِدَ وَلَآ ءَآمِّينَ ٱلۡبَيۡتَ ٱلۡحَرَامَ يَبۡتَغُونَ فَضۡلٗا مِّن رَّبِّهِمۡ وَرِضۡوَٰنٗاۚ وَإِذَا حَلَلۡتُمۡ فَٱصۡطَادُواْۚ وَلَا يَجۡرِمَنَّكُمۡ شَنَـَٔانُ قَوۡمٍ أَن صَدُّوكُمۡ عَنِ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ أَن تَعۡتَدُواْۘ وَتَعَاوَنُواْ عَلَى ٱلۡبِرِّ وَٱلتَّقۡوَىٰۖ وَلَا تَعَاوَنُواْ عَلَى ٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡعُدۡوَٰنِۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَۖ إِنَّ ٱللَّهَ شَدِيدُ ٱلۡعِقَابِ

E inu amene mwakhulupirira! Musanyozere kupatulika kwa zizindikiro za Allah (pochiyesa chosapatulika chomwe Allah wachichita kukhala chopatulika; monga kutuluka m’mapemphero a Hajj usadakwaniritse), kapenanso (kunyozera) kupatulika kwa mwezi wopatulika (poyambitsa nkhondo mmenemo), kapena (kupatulika kwa nyama zomwe zatumizidwa ku Makka monga) nsembe, kapena (kuchotsa kupatulika kwa) makoza (omwe nyamazo zimavekedwa monga chizindikiro chosonyeza kuti ndinsembe ya ku Makka), kapena (kupatulika kwa) omwe akulinga kupita kunyumba yopatulika (ku Makka), (omwe akupita kumeneko) ndi cholinga chofunafuna ubwino wa Mbuye wawo ndi chiyanjo Chake. Ndipo ngati mutatuluka m’mapemphero anu a Hajj mukhoza kuchita ulenje (ngati mutafuna); ndipo kusakuchititseni kuwada anthu chifukwa chakuti adakutsekerezani kufika ku Msikiti Wopatulika (wa ku Makka) kuti mulumphe malire (pobwezera mtopola umene adakuchitirani). Koma thandizanani pa zabwino ndikuopa (Allah); musathandizane pa machimo ndi pa chidani. Ndipo muopeni Allah. Ndithu Allah Ngwaukali pokhaulitsa. info
التفاسير: