Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - Die Übersetzung in Chichewa - Khalid Ibrahim Bityala.

Nummer der Seite:close

external-link copy
84 : 5

وَمَا لَنَا لَا نُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ وَمَا جَآءَنَا مِنَ ٱلۡحَقِّ وَنَطۡمَعُ أَن يُدۡخِلَنَا رَبُّنَا مَعَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلصَّٰلِحِينَ

(Atadzudzulidwa polowa m’Chisilamu iwo adati): “Chifukwa ninji tisamkhulupirire Allah ndi choonadi chomwe chatifika, pomwe tikuyembekezera Mbuye wathu kukatilowetsa (ku Munda wamtendere) pamodzi ndi anthu abwino?” info
التفاسير:

external-link copy
85 : 5

فَأَثَٰبَهُمُ ٱللَّهُ بِمَا قَالُواْ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ وَذَٰلِكَ جَزَآءُ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Choncho Allah adzawalipira, pa zomwe adanena, Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali. Imeneyo ndiyo mphoto ya ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
86 : 5

وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَآ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَحِيمِ

Ndipo amene sadakhulipirire, nkutsutsa zizindikiro zathu, iwowo ndiwo anthu a ku Moto. info
التفاسير:

external-link copy
87 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تُحَرِّمُواْ طَيِّبَٰتِ مَآ أَحَلَّ ٱللَّهُ لَكُمۡ وَلَا تَعۡتَدُوٓاْۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ ٱلۡمُعۡتَدِينَ

E inu amene mwakhulupirira! Musazichite zabwino zomwe Allah wakulolezani kukhala zoletsedwa. Ndipo musalumphe malire, ndithudi Allah sakonda anthu olumpha malire. info
التفاسير:

external-link copy
88 : 5

وَكُلُواْ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُ حَلَٰلٗا طَيِّبٗاۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ ٱلَّذِيٓ أَنتُم بِهِۦ مُؤۡمِنُونَ

Idyani zabwino zomwe Allah wakupatsani zomwe zili zololedwa. Ndipo opani Allah yemwe inu mukumkhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
89 : 5

لَا يُؤَاخِذُكُمُ ٱللَّهُ بِٱللَّغۡوِ فِيٓ أَيۡمَٰنِكُمۡ وَلَٰكِن يُؤَاخِذُكُم بِمَا عَقَّدتُّمُ ٱلۡأَيۡمَٰنَۖ فَكَفَّٰرَتُهُۥٓ إِطۡعَامُ عَشَرَةِ مَسَٰكِينَ مِنۡ أَوۡسَطِ مَا تُطۡعِمُونَ أَهۡلِيكُمۡ أَوۡ كِسۡوَتُهُمۡ أَوۡ تَحۡرِيرُ رَقَبَةٖۖ فَمَن لَّمۡ يَجِدۡ فَصِيَامُ ثَلَٰثَةِ أَيَّامٖۚ ذَٰلِكَ كَفَّٰرَةُ أَيۡمَٰنِكُمۡ إِذَا حَلَفۡتُمۡۚ وَٱحۡفَظُوٓاْ أَيۡمَٰنَكُمۡۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمۡ ءَايَٰتِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ

Allah sangakulangeni chifukwa chakulumbira kwanu kopanda pake. Koma akulangani kamba ka malumbiro omwe mwalumbira motsimikiza. Choncho dipo lake ndikuwadyetsa osauka khumi ndi chakudya cha mlingo wapakatikati chomwe mumawadyetsa anthu anu; kapena kuwaveka, kapena kumpatsa ufulu kapolo. Koma amene sangapeze zimenezo, asale masiku atatu. Ili ndi dipo la kulumbira kwanu pamene mukulumbira. Ndipo sungani malumbilo anu, (musaswe chomwe mudalumbilira). Motero ndi momwe Allah akukufotokozerani zizindikiro Zake kuti muthokoze. info
التفاسير:

external-link copy
90 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِنَّمَا ٱلۡخَمۡرُ وَٱلۡمَيۡسِرُ وَٱلۡأَنصَابُ وَٱلۡأَزۡلَٰمُ رِجۡسٞ مِّنۡ عَمَلِ ٱلشَّيۡطَٰنِ فَٱجۡتَنِبُوهُ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ

E inu amene mwakhulupirira! Ndithudi, mowa (kutchova) njuga, kupembedza mafano ndi kuombeza maula, (zonsezi) ndi uve, mwa ntchito za satana. Choncho zipeweni kuti mupambane. info
التفاسير: