[155] Chisilamu chimalemekeza zinthu zogwilira ntchito ya chipembedzo, monga ziweto zimene amazitumiza ku Makka ncholinga choti akazizinge kumeneko monga sadaka yopereka konko. Ndipo anthu okachita mapemphero a Hajjiwo, ziweto amaziveka zizindikiro zosonyeza kuti nziweto zomwe akukazipereka monga nsembe kwa Allah. Ndipo nyamazo zimakhala zopatulika. Choncho sibwino kuswa kupatulika kumeneku pozilanda mwachifwamba ndi kuzipha zisanafike pamalo pake poziphera.