Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
98 : 18

قَالَ هَٰذَا رَحۡمَةٞ مِّن رَّبِّيۖ فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ رَبِّي جَعَلَهُۥ دَكَّآءَۖ وَكَانَ وَعۡدُ رَبِّي حَقّٗا

(Iye) adati: “Ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wanga; koma likadzafika lonjezo la Mbuye wanga (kudza kwa Qiyâma), adzachiswanyaswanya; ndipo lonjezo la Mbuye wanga nloona.” info
التفاسير:

external-link copy
99 : 18

۞ وَتَرَكۡنَا بَعۡضَهُمۡ يَوۡمَئِذٖ يَمُوجُ فِي بَعۡضٖۖ وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَجَمَعۡنَٰهُمۡ جَمۡعٗا

Ndipo patsiku limenelo tidzawasiya ena a iwo (oipa) akuchita chipolowe pa ena; ndipo lidzaimbidwa lipenga. Pamenepo tidzawasonkhanitsa onse pamodzi. info
التفاسير:

external-link copy
100 : 18

وَعَرَضۡنَا جَهَنَّمَ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡكَٰفِرِينَ عَرۡضًا

Ndipo tsiku limenelo, tidzayionetsa poyera Jahannam kwa osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
101 : 18

ٱلَّذِينَ كَانَتۡ أَعۡيُنُهُمۡ فِي غِطَآءٍ عَن ذِكۡرِي وَكَانُواْ لَا يَسۡتَطِيعُونَ سَمۡعًا

(Osakhulupirira) omwe maso awo adali ophimbidwa pakusalabadira ulaliki Wanga, ndipo sadali kutha kumva (zimene akuuzidwa). info
التفاسير:

external-link copy
102 : 18

أَفَحَسِبَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَن يَتَّخِذُواْ عِبَادِي مِن دُونِيٓ أَوۡلِيَآءَۚ إِنَّآ أَعۡتَدۡنَا جَهَنَّمَ لِلۡكَٰفِرِينَ نُزُلٗا

Kodi osakhulupirira akuganiza kuti angawasandutse akapolo Anga kukhala atetezi kusiya Ine? Ndithu taikonza Jahannam kukhala malo ofikirapo osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
103 : 18

قُلۡ هَلۡ نُنَبِّئُكُم بِٱلۡأَخۡسَرِينَ أَعۡمَٰلًا

Nena: “Kodi tikudziwitseni eni kuluza (kulephera) pa zochita zawo?” info
التفاسير:

external-link copy
104 : 18

ٱلَّذِينَ ضَلَّ سَعۡيُهُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَهُمۡ يَحۡسَبُونَ أَنَّهُمۡ يُحۡسِنُونَ صُنۡعًا

“Iwo ndi omwe khama lawo lataika m’moyo wa pa dziko lapansi, pomwe iwowo akuganiza kuti akuchita zabwino”.[263] info

[263] M’ndime iyi akutiuza kuti amene sadakhulupirire Allah, pa tsiku lachimaliziro ndiye kuti zonse zochita zawo zidzakhala zowonongeka. Ntchito zabwino za munthu kuti zikalandiridwe kwa Allah, poyamba akhulupirire Allah ndiponso akhulupirire kuti tsiku lachimaliziro lilipo. Koma ngati sakhulupilira, ndiye kuti zochita zake sizikayesedwa pasikelo koma akangomponya kung’anjo yamoto. Pankhaniyi Mtumiki (s.a.w) adati: “Tsiku la Qiyâma padzabwera munthu wamtali, wakudyabwino, wakumwa zomwaimwa, koma kwa Allah adzakhala wopepuka wosafanana ngakhale ndikulemera kwa phiko la udzudzu.” Hadisiyi adainena ndi Al -Hafizi Ibn Hajar m’buku la Fatuhul Bari, Volume 8 tsamba la 324.

التفاسير:

external-link copy
105 : 18

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ وَلِقَآئِهِۦ فَحَبِطَتۡ أَعۡمَٰلُهُمۡ فَلَا نُقِيمُ لَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَزۡنٗا

Iwowo ndi amene sadakhulupirire zisonyezo za Mbuye wawo, ndipo (sadakhulupirire) zakukumana Naye. Choncho zochita zawo zaonongeka (zapita pachabe), ndipo pa tsiku la chiweruziro sitidzawaikira sikelo. info
التفاسير:

external-link copy
106 : 18

ذَٰلِكَ جَزَآؤُهُمۡ جَهَنَّمُ بِمَا كَفَرُواْ وَٱتَّخَذُوٓاْ ءَايَٰتِي وَرُسُلِي هُزُوًا

Zimenezo, mphoto yawo ndi Jahannam chifukwa cha kusakhulupirira kwawo, ndipo Ayah Zanga ndi atumiki Anga adazichitira chipongwe. info
التفاسير:

external-link copy
107 : 18

إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ كَانَتۡ لَهُمۡ جَنَّٰتُ ٱلۡفِرۡدَوۡسِ نُزُلًا

Ndithu amene akhulupirira ndikumachita zabwino, malo awo ofikira adzakhala ku minda ya “Firdaus.” info
التفاسير:

external-link copy
108 : 18

خَٰلِدِينَ فِيهَا لَا يَبۡغُونَ عَنۡهَا حِوَلٗا

Adzakhalamo nthawi yaitali. Ndipo sadzafuna kuchokamo. info
التفاسير:

external-link copy
109 : 18

قُل لَّوۡ كَانَ ٱلۡبَحۡرُ مِدَادٗا لِّكَلِمَٰتِ رَبِّي لَنَفِدَ ٱلۡبَحۡرُ قَبۡلَ أَن تَنفَدَ كَلِمَٰتُ رَبِّي وَلَوۡ جِئۡنَا بِمِثۡلِهِۦ مَدَدٗا

Nena: “Ngakhale nyanja ikadakhala inki yolembera mawu a Mbuye wanga, nyanjayo ikadatha mawu a Mbuye wanga asadathe, ngakhale tikadabweretsa nyanja ina ndikuionjezera pa iyo (nyanjazo zikadatha, mawu a Allah akalipobe).” info
التفاسير:

external-link copy
110 : 18

قُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ بَشَرٞ مِّثۡلُكُمۡ يُوحَىٰٓ إِلَيَّ أَنَّمَآ إِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞۖ فَمَن كَانَ يَرۡجُواْ لِقَآءَ رَبِّهِۦ فَلۡيَعۡمَلۡ عَمَلٗا صَٰلِحٗا وَلَا يُشۡرِكۡ بِعِبَادَةِ رَبِّهِۦٓ أَحَدَۢا

Nena: “Ndithu ine ndi munthu monga inu, (chosiyana nchakuti) ine ndikupatsidwa chivumbulutso (chonena kuti) ndithu Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi Yekha. Ndipo amene afuna kukumana ndi Mbuye wake, achite zochita zabwino ndipo asaphatikizepo aliyense pa mapemphero a Mbuye wake.” info
التفاسير: