Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
84 : 18

إِنَّا مَكَّنَّا لَهُۥ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَءَاتَيۡنَٰهُ مِن كُلِّ شَيۡءٖ سَبَبٗا

Ndithu tidampatsa mphamvu zokhalira pa dziko ndikumpatsa njira yopezera chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
85 : 18

فَأَتۡبَعَ سَبَبًا

Choncho adatsata njira. info
التفاسير:

external-link copy
86 : 18

حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغَ مَغۡرِبَ ٱلشَّمۡسِ وَجَدَهَا تَغۡرُبُ فِي عَيۡنٍ حَمِئَةٖ وَوَجَدَ عِندَهَا قَوۡمٗاۖ قُلۡنَا يَٰذَا ٱلۡقَرۡنَيۡنِ إِمَّآ أَن تُعَذِّبَ وَإِمَّآ أَن تَتَّخِذَ فِيهِمۡ حُسۡنٗا

Mpaka pomwe adafika kumlowero kwa dzuwa (ku maiko a kuzambwe), adaliona (ngati) likulowa pa dziwe la matope ambiri. Ndipo pompo adapeza anthu; tidati: “E iwe Thul-Qarnain! Alange, kapena achitire zabwino.” info
التفاسير:

external-link copy
87 : 18

قَالَ أَمَّا مَن ظَلَمَ فَسَوۡفَ نُعَذِّبُهُۥ ثُمَّ يُرَدُّ إِلَىٰ رَبِّهِۦ فَيُعَذِّبُهُۥ عَذَابٗا نُّكۡرٗا

Adati: “Koma amene achita zosalungama timulanga; ndipo kenako adzabwezedwa kwa Mbuye wake; ndipo akamukhaulitsa ndi chilango choipa. info
التفاسير:

external-link copy
88 : 18

وَأَمَّا مَنۡ ءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗا فَلَهُۥ جَزَآءً ٱلۡحُسۡنَىٰۖ وَسَنَقُولُ لَهُۥ مِنۡ أَمۡرِنَا يُسۡرٗا

Koma amene akhulupirire ndikuchita ntchito zabwino, apeza mphoto yabwino; ndipo timuuza zomwe zili zofewa m’zinthu zathu.” info
التفاسير:

external-link copy
89 : 18

ثُمَّ أَتۡبَعَ سَبَبًا

Kenako adatsata njira. info
التفاسير:

external-link copy
90 : 18

حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغَ مَطۡلِعَ ٱلشَّمۡسِ وَجَدَهَا تَطۡلُعُ عَلَىٰ قَوۡمٖ لَّمۡ نَجۡعَل لَّهُم مِّن دُونِهَا سِتۡرٗا

Mpaka adafika ku mtulukiro kwa dzuwa (ku maiko akuvuma). Adalipeza (dzuwalo) likuwatulukira anthu omwe sitidawaikire chowatchinga ku ilo. info
التفاسير:

external-link copy
91 : 18

كَذَٰلِكَۖ وَقَدۡ أَحَطۡنَا بِمَا لَدَيۡهِ خُبۡرٗا

Momwemo, tidali kudziwa bwino nkhani zonse zomwe zidali ndi iye. info
التفاسير:

external-link copy
92 : 18

ثُمَّ أَتۡبَعَ سَبَبًا

Kenako adatsata njira. info
التفاسير:

external-link copy
93 : 18

حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغَ بَيۡنَ ٱلسَّدَّيۡنِ وَجَدَ مِن دُونِهِمَا قَوۡمٗا لَّا يَكَادُونَ يَفۡقَهُونَ قَوۡلٗا

Mpaka pomwe adafika pakatikati pa mapiri awiri adapeza pafupi ndi mapiriwo anthu omwe sikudali kwapafupi kumva chiyankhulo. info
التفاسير:

external-link copy
94 : 18

قَالُواْ يَٰذَا ٱلۡقَرۡنَيۡنِ إِنَّ يَأۡجُوجَ وَمَأۡجُوجَ مُفۡسِدُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَهَلۡ نَجۡعَلُ لَكَ خَرۡجًا عَلَىٰٓ أَن تَجۡعَلَ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَهُمۡ سَدّٗا

Adati: “E iwe Zul-Qarnain! Ndithu Yaajuju ndi Maajuju akuononga pa dziko. Kodi sikungatheke kuti tikupatse malipiro kuti uike pakati pathu ndi pakati pawo, chotchinga (mpanda)?” info
التفاسير:

external-link copy
95 : 18

قَالَ مَا مَكَّنِّي فِيهِ رَبِّي خَيۡرٞ فَأَعِينُونِي بِقُوَّةٍ أَجۡعَلۡ بَيۡنَكُمۡ وَبَيۡنَهُمۡ رَدۡمًا

(Iye) adati: “Zomwe Mbuye wanga wandipatsa ndi zabwino. Choncho ndithandizeni ndi mphamvu zanu (zonse pantchito imeneyi) ndiika chotchinga cholimba pakati panu ndi pakati pawo.” info
التفاسير:

external-link copy
96 : 18

ءَاتُونِي زُبَرَ ٱلۡحَدِيدِۖ حَتَّىٰٓ إِذَا سَاوَىٰ بَيۡنَ ٱلصَّدَفَيۡنِ قَالَ ٱنفُخُواْۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَعَلَهُۥ نَارٗا قَالَ ءَاتُونِيٓ أُفۡرِغۡ عَلَيۡهِ قِطۡرٗا

“Ndipatseni zidutswa za zitsulo.” Kufikira pamene adadzaza ndi zitsulozo mpata umene udalipo pakati pa mapiri awiriwo, adati: “Pemelerani (moto).” Mpaka (chitsulocho) chidafiira monga moto, adati: “Ndibweretsereni mtovu wosungunuka ndiuthire pamwamba pake (pa chitsulocho).” info
التفاسير:

external-link copy
97 : 18

فَمَا ٱسۡطَٰعُوٓاْ أَن يَظۡهَرُوهُ وَمَا ٱسۡتَطَٰعُواْ لَهُۥ نَقۡبٗا

Choncho (Yaajuju ndi Maajuju) sadathe kukwera pamwamba pake, ndiponso sadathe kuchiboola. info
التفاسير: