Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
75 : 18

۞ قَالَ أَلَمۡ أَقُل لَّكَ إِنَّكَ لَن تَسۡتَطِيعَ مَعِيَ صَبۡرٗا

۞ Adati: “Kodi sindidakuuze (kuti) ndithu iwe sutha kupirira nane?” info
التفاسير:

external-link copy
76 : 18

قَالَ إِن سَأَلۡتُكَ عَن شَيۡءِۭ بَعۡدَهَا فَلَا تُصَٰحِبۡنِيۖ قَدۡ بَلَغۡتَ مِن لَّدُنِّي عُذۡرٗا

(Mûsa) adati: “Ngati ndikufunsanso chilichonse pambuyo pa ichi, usandilole kutsagana nawe. Ndiye kuti wakwaniritsa dandaulo lako pa ine.” info
التفاسير:

external-link copy
77 : 18

فَٱنطَلَقَا حَتَّىٰٓ إِذَآ أَتَيَآ أَهۡلَ قَرۡيَةٍ ٱسۡتَطۡعَمَآ أَهۡلَهَا فَأَبَوۡاْ أَن يُضَيِّفُوهُمَا فَوَجَدَا فِيهَا جِدَارٗا يُرِيدُ أَن يَنقَضَّ فَأَقَامَهُۥۖ قَالَ لَوۡ شِئۡتَ لَتَّخَذۡتَ عَلَيۡهِ أَجۡرٗا

Choncho adamuka; kufikira pamene adawapeza eni mudzi ndipo adawapempha eni mudziwo chakudya, koma adakana kuwalandira monga alendo. Ndipo adapezamo khoma lili pafupi kugwa, (ndipo Khidhiriyo) adaliimika. (Mûsa) adati: “Ngati ukadafuna, ukadalandira malipiro (pa ntchitoyi kuti tigulire chakudya).” info
التفاسير:

external-link copy
78 : 18

قَالَ هَٰذَا فِرَاقُ بَيۡنِي وَبَيۡنِكَۚ سَأُنَبِّئُكَ بِتَأۡوِيلِ مَا لَمۡ تَسۡتَطِع عَّلَيۡهِ صَبۡرًا

(Khidhiri) adati: “Awa ndiwo malekano pakati pa ine ndi iwe. Tsopano ndikuuza tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”[261] info

[261] Mtumiki Muhammad (s.a.w) adati pankhani iyi ya Musa ndi Khidhiri: “Allah amchitire chifundo Musa. Ndikulakalaka kuti iye akadapilira kukhala limodzi ndi mnzakeyo, akadaona zodabwitsa, ndipo Allah akadatisimbira zambiri za iwo.”

التفاسير:

external-link copy
79 : 18

أَمَّا ٱلسَّفِينَةُ فَكَانَتۡ لِمَسَٰكِينَ يَعۡمَلُونَ فِي ٱلۡبَحۡرِ فَأَرَدتُّ أَنۡ أَعِيبَهَا وَكَانَ وَرَآءَهُم مَّلِكٞ يَأۡخُذُ كُلَّ سَفِينَةٍ غَصۡبٗا

“Tsopano chombo chija, chidali cha masikini ogwira ntchito pa nyanja, ndipo ndidafuna kuchiononga (mwadala) chifukwa patsogolo pawo padali mfumu yomwe imatenga chombo chilichonse (chabwino) molanda.” info
التفاسير:

external-link copy
80 : 18

وَأَمَّا ٱلۡغُلَٰمُ فَكَانَ أَبَوَاهُ مُؤۡمِنَيۡنِ فَخَشِينَآ أَن يُرۡهِقَهُمَا طُغۡيَٰنٗا وَكُفۡرٗا

“Ndipo mnyamata uja, makolo ake adali okhulupirira, ndipo tidaopera kuti angawachititse zoipa (makolo akewo) ndi za kusakhulupirira (mwa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
81 : 18

فَأَرَدۡنَآ أَن يُبۡدِلَهُمَا رَبُّهُمَا خَيۡرٗا مِّنۡهُ زَكَوٰةٗ وَأَقۡرَبَ رُحۡمٗا

Choncho tidafuna kuti Mbuye wawo awasinthire ndi wabwino kuposa iye pa kuyera, ndi wachifundo chapafupi (kwa makolo ake.)” info
التفاسير:

external-link copy
82 : 18

وَأَمَّا ٱلۡجِدَارُ فَكَانَ لِغُلَٰمَيۡنِ يَتِيمَيۡنِ فِي ٱلۡمَدِينَةِ وَكَانَ تَحۡتَهُۥ كَنزٞ لَّهُمَا وَكَانَ أَبُوهُمَا صَٰلِحٗا فَأَرَادَ رَبُّكَ أَن يَبۡلُغَآ أَشُدَّهُمَا وَيَسۡتَخۡرِجَا كَنزَهُمَا رَحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَۚ وَمَا فَعَلۡتُهُۥ عَنۡ أَمۡرِيۚ ذَٰلِكَ تَأۡوِيلُ مَا لَمۡ تَسۡطِع عَّلَيۡهِ صَبۡرٗا

“Tsopano chipupa chija, chidali cha ana awiri amasiye mu mzindamo; ndipo pansi pake padali chuma chawo (chimene adawasiira bambo wawo) ndipo tate wawo adali munthu wabwino choncho Mbuye wako adafuna kuti akule misinkhu yawo ndipo adzadzitulutsire chuma chawocho; ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo ine sindidachite zinthu zimenezi mwandekha. Limenelo ndilo tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”[262] info

[262] Nkhani ya Musa ndi Al-Khidhiri yomwe ikupezeka mu Sahihi Bukhari ndi Muslim, Ubayu bun Kaabi adailandira kuchokera kwa Mtumiki wa Allah (s.a.w) kuti iye adati: “Ndithudi, Musa adaimilira kulalikira kwa ana a Isiraeli, ndipo adamufunsa kuti: “Ndani mwa anthu yemwe ngodziwa kwambiri?” Iye adati: “Ndine.” Ndipo Allah adamudzudzula pa yankho lake lotere. Choncho Allah adamuzindikiritsa iye nati: “Ndithu ine ndilinaye kapolo pamajiga panyanja ziwiri yemwe ngodziwa kwambiri kuposa iwe”.
Musa adati: “E Mbuye wanga! Ndingampeze bwanji iyeyo”? Allah adati: ‘Tenga nsomba, uiike muswanda (Basikete). Pamene nsombayo ikakusowe, ndiye kuti iye ali pamenepo.” Tero Musa pamodzi ndi mnyamata wake (Yusha Bun Nun) adaubutsa ulendo mpaka kukafika pa thanthwe. Adasamiritsa mitu yawo pamenepo mpaka kugona tulo. Ndipo nsomba idapiripita m’swanda muja, nkutuluka kukagwera mnyanja. Koma Allah adamanga kuyenda kwa madzi pamene nsombayo idagwera adangounjikana chimulu pompo.
Pamene adauka, mnyamata uja adaiwala kumuuza za nsombayo, naayenda usana ndi usiku kufikira mmawa mwake mwa tsiku limenelo. Musa adati kwa mnyamata wake, “Tipatseni chakudya chathu cham’mawa; ndithu tapeza zotopetsa pa ulendo wathupa.” Adati Musa sadamve kutopa kufikira pamene adadutsa pamalo pomwe Allah adamulamulapo. Mnyamata wake adati: “Kodi mwaona? Titafika pathanthwe ine ndidaiwala nkhani ya nsomba ija. Komatu palibe amene wandiiwalitsa kuikumbukira, koma satana basi. Idatenga njira yake kunka m’nyanja mododometsa.” Musa adati: “Pamenepo mpomwe timafuna.” Choncho adabwerera kulondola mapazi awo mpaka kukafika pathanthwe lija. Apo adaona munthu atadzifundika nsalu. Musa adampatsa salaamu, ndipo Al-Khidhiri adati: “Yachokera kuti salaamu yotere m’dziko lako! Kodi ndiwe yani? Adati “Ine ndine Musa.” Iye adati Musa wa ana a Isiraeli?” Musa adavomera kuti inde, ndadza kuti mundiphunzitse zomwe mwaphunzitsidwa za chiongoko.” Munthu uja adati: “Ndithudi, iwe suutha kupilira nane chifukwa ine ndili ndi maphunziro anga omwe Allah wandiphunzitsa, amene iwe sukuwadziwa.” Musa adati; “Undipeza ndili wopilira ngati Allah afuna. Sindinyoza chilichonse cha iwe. Al-Khidhiri adati kwa iye: “Ngati unditsatedi usandifunse kufikira nditakufotokozera.” Choncho onse awiri adachoka nayenda m’mphepete mwanyanja. Chidawadutsa chombo ndipo adawalankhula eni chombowo kuti awanyamule. Eni chombowo adamdziwa Al-Khidhiri ndipo adawanyamula popanda malipiro. Atakwera m’chombomo Al-Khidhiri adagulula thabwa la chombocho ndi nkhwangwa.
Musa adati: “Nchiyani ichi; anthuwa atitenga popanda malipiro ndiye ukuboola chombo chawo? Kodi ukufuna kuti uwamize eni chombowo? Ndithudi, wachita chinthu choipa kwambiri.” Kenaka adachoka m’chombo muja nayamba kuyenda m’phepete mwanyanja. Pompo Al-Khidhiri adaona mwana akusewera ndi mzake ndipo adamgwira mwana uja mutu wake ndikuuzula, nkumpheratu. Musa adati kwa iye: “Bwanji wapha munthu wosalakwa yemwe sadaphe munthu mnzake? Ndithu wachita chinthu chonyansa kwabasi,”. Munthu uja adati; “Kodi sindidakuuze kuti sutha kupilira nane”? Musa adati: “Ngati ndikufunsanso chinthu china pambuyo pa ichi, usandilole kutsagana nawe. Apo tsono ndiye kuti kundidandaula kwako kwakwanira pa ine.” Tero adachoka mpaka kufika pamudzi wina. Apo adapempha chakudya kwa eni mudziwo. Adakana kuwalandira monga alendo. Ndipo kenaka adapeza khorna lili pafupi kugwa, Al-Khidhiri adati ndi mkono wake “Ima chonchi,” - polilozera ndi mkono wake. Ndipo lidaimadi njoo!. Musa adati: “Ha! Anthu akuti tawadzera pamudzi, ndipo sanatipatse chakudya sanatilandirenso ngati alendo! Apatu ukadafuna ukadaitanitsa malipiro.” Munthu uja adati: “Awa ndiwo malekano a iwe ndi ine. Komabe ndikuuza matanthauzo a zomwe sudathe kupilira nazo.”
Izi ndi zina zododometsa za Allah zomwe amazichita kupyolera m’manja mwa anthu ake olungama. Ngati tidzakhala olungama ndiye kuti Allah adzatipatsa mphamvu zochita zinthu zododometsa.

التفاسير:

external-link copy
83 : 18

وَيَسۡـَٔلُونَكَ عَن ذِي ٱلۡقَرۡنَيۡنِۖ قُلۡ سَأَتۡلُواْ عَلَيۡكُم مِّنۡهُ ذِكۡرًا

Ndipo akukufunsa nkhani za Thul-Qarnain. Auze: “Ndikulakatulirani zina mwa nkhani zake.” info
التفاسير: