Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ.

Al-Anfâl

external-link copy
1 : 8

يَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلۡأَنفَالِۖ قُلِ ٱلۡأَنفَالُ لِلَّهِ وَٱلرَّسُولِۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَصۡلِحُواْ ذَاتَ بَيۡنِكُمۡۖ وَأَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥٓ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ

Akukufunsa za chuma cholandidwa pa nkhondo (mmene chingagawidwire). Nena: “Chuma cholanda pa nkhondo ndi cha Allah ndi Mtumiki (ndiamene ali olamula kagawidwe kake); choncho, muopeni Allah ndipo yanjanani mwachibale pakati panu. Mverani Allah ndi Mtumiki Wake, ngati mulidi okhulupirira.”[189] info

[189] Nkhondo ya Chisilamu ndinkhondo yomenyera kuti chipembedzo cha Chisilamu chisafafanizidwe ndi anthu ochida. Osati chifukwa chofuna kupeza chuma. Asilamu adafunsa Mtumiki za kagawidwe ka chuma cholanda pankhondo ndipo anauzidwa kuti chuma cha pa nkhondo ncha Allah ndi Mtumiki ndiamenenso angachigawe pakati pa Asilamu.

التفاسير:

external-link copy
2 : 8

إِنَّمَا ٱلۡمُؤۡمِنُونَ ٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِرَ ٱللَّهُ وَجِلَتۡ قُلُوبُهُمۡ وَإِذَا تُلِيَتۡ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُهُۥ زَادَتۡهُمۡ إِيمَٰنٗا وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ

Ndithu okhulupirira, enieni ndi amene akuti Allah akatchulidwa mitima yawo imadzadzidwa ndi mantha; pamenenso Ayah Zake zikuwerengedwa kwa iwo zimawaonjezera chikhulupiliro, ndipo amayadzamira kwa Mbuye wawo Yekha basi; (sakhulupirira nyanga ndi mizimu ya anthu akufa).[190] info

[190] Apa patchulidwa ena mwa makhalidwe a Asilamu omwe ngokwanira pachikhulupiliro chawo. Amene alibe makhalidwe otere, ndiye kuti chikhulupiliro chawo nchosakwanira ndipo pa tsiku la chimaliziro sichidzawapindulira zabwino.

التفاسير:

external-link copy
3 : 8

ٱلَّذِينَ يُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ

Amene amaimilira kupemphera napereka chimene tawapatsa, (pa njira ya Allah, ndikuthandiza ovutika). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 8

أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ حَقّٗاۚ لَّهُمۡ دَرَجَٰتٌ عِندَ رَبِّهِمۡ وَمَغۡفِرَةٞ وَرِزۡقٞ كَرِيمٞ

Awa (okhala ndi makhalidwe otere) ndi amene ali okhulupirira mwachoonadi. Iwo adzapeza ulemelero (wapamwamba) kwa Mbuye wawo, ndi chikhululuko ndi zopatsidwa zaulemu. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 8

كَمَآ أَخۡرَجَكَ رَبُّكَ مِنۢ بَيۡتِكَ بِٱلۡحَقِّ وَإِنَّ فَرِيقٗا مِّنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ لَكَٰرِهُونَ

Monga mmene Mbuye wako adakulamulira kutuluka m’nyumba yako (kupita ku Badr kukachita nkhondo ndi osakhulupirira) mwachoonadi, ndithu gulu lina la okhulipirira silidafune (kuchoka kukakumana ndi adani).[191] info

[191] Pamene Asilamu adauzidwa kukakumana ndi Aquraish kuti akamenyane nawo nkhondo, ena mwa Asilamu adachita mantha chifukwa chakuti nthawiyi idali yoyamba kwa iwo kuuzidwa zokamenyana ndi adani awo, poganiziranso kuti Aquraish adali akatswiri pomenya nkhondo, ndiponso adali ochuluka zedi kuposa iwo. Choncho Asilamu adayesera kupereka madandaulo awa ndi awa.

التفاسير:

external-link copy
6 : 8

يُجَٰدِلُونَكَ فِي ٱلۡحَقِّ بَعۡدَ مَا تَبَيَّنَ كَأَنَّمَا يُسَاقُونَ إِلَى ٱلۡمَوۡتِ وَهُمۡ يَنظُرُونَ

Akutsutsana nawe (pa chinthu) choona pambuyo pakuti chaonekera poyera. (Kukuwaipira kukumana ndi adani) ngati kuti akubusidwa kunka ku imfa akuona. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 8

وَإِذۡ يَعِدُكُمُ ٱللَّهُ إِحۡدَى ٱلطَّآئِفَتَيۡنِ أَنَّهَا لَكُمۡ وَتَوَدُّونَ أَنَّ غَيۡرَ ذَاتِ ٱلشَّوۡكَةِ تَكُونُ لَكُمۡ وَيُرِيدُ ٱللَّهُ أَن يُحِقَّ ٱلۡحَقَّ بِكَلِمَٰتِهِۦ وَيَقۡطَعَ دَابِرَ ٱلۡكَٰفِرِينَ

(Kumbukirani, E inu okhulupirira!) Pamene Allah anakulonjezani gulu limodzi mwa magulu awiri kuti likhale lanu (kuti mumenyane nalo). Koma inu mukufuna lopanda mphamvu kuti likhale lanu (kuti ndilo mumenyane nalo). Koma Allah akufuna kuchitsimikiza choonadi ndi mawu Ake ndi kudula mizu ya osakhulupirira, (pomenyana ndi gulu lamphamvulo, omwe ndi ankhondo a Chikuraishi). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 8

لِيُحِقَّ ٱلۡحَقَّ وَيُبۡطِلَ ٱلۡبَٰطِلَ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡمُجۡرِمُونَ

Kuti achitsimikizire choonadi ndi kulichotsa bodza; ngakhale zikuwaipira anthu oipa. info
التفاسير: