[189] Nkhondo ya Chisilamu ndinkhondo yomenyera kuti chipembedzo cha Chisilamu chisafafanizidwe ndi anthu ochida. Osati chifukwa chofuna kupeza chuma. Asilamu adafunsa Mtumiki za kagawidwe ka chuma cholanda pankhondo ndipo anauzidwa kuti chuma cha pa nkhondo ncha Allah ndi Mtumiki ndiamenenso angachigawe pakati pa Asilamu.
[190] Apa patchulidwa ena mwa makhalidwe a Asilamu omwe ngokwanira pachikhulupiliro chawo. Amene alibe makhalidwe otere, ndiye kuti chikhulupiliro chawo nchosakwanira ndipo pa tsiku la chimaliziro sichidzawapindulira zabwino.
[191] Pamene Asilamu adauzidwa kukakumana ndi Aquraish kuti akamenyane nawo nkhondo, ena mwa Asilamu adachita mantha chifukwa chakuti nthawiyi idali yoyamba kwa iwo kuuzidwa zokamenyana ndi adani awo, poganiziranso kuti Aquraish adali akatswiri pomenya nkhondo, ndiponso adali ochuluka zedi kuposa iwo. Choncho Asilamu adayesera kupereka madandaulo awa ndi awa.