E inu ana a Adam! Tengani (valani) zovala zanu zabwino pamene mukukapemphera Swala iliyonse ndipo idyani ndi kumwa; koma musapyoze muyeso. Iye (Allah) sakonda opyoza muyeso (oononga).
Nena: “Ndani waletsa zokongoletsa za Allah (zovala), zomwe Iye (Allah) adawatulutsira akapolo Ake ndi zakudya zabwino?” Nena: “Zinthu zimenezo nzololedwa kwa amene akhulupirira (Asilamu) pamoyo wa pa dziko lapansi. (Zidzakhala) zawozawo tsiku la chimaliziro. M’menemo ndi momwe tikulongosolera Ayah (Zathu) kwa anthu ozindikira.”[181]
[181] Padali anthu ena omwe adali ndi chikhulupiliro choti kuvala nsanza ndi kudya zinthu zosakoma ndiko kumuopa Allah. Mpaka masiku ano alipobe anthu oganiza motere. Ndipo nchifukwa chake Allah akuvumbulutsa Ayah izi kuti kutero sindiko kumuopa Allah.
Nena (kwa iwo): “Ndithu Mbuye wanga waletsa zinthu zauve zoonekera ndi zobisika, ndi machimo, ndi kuwukira (atsogoleri) popanda choonadi, ndi kumphatikiza Allah ndi chomwe sadachitsitsire umboni (wakuti chiphatikizidwe ndi Iye); ndiponso (waletsa) kumunenera Allah zimene simukuzidziwa.”[182]
[182] Choipa nchoipa basi. Kaya kuchichita moonekera kapena mobisa, nchoipabe.
E inu ana a Adam! Akakudzerani Atumiki ochokera mwa inu namakuuzani zivumbulutso Zanga, (avomereni), choncho omwe adzitchinjiriza ku zoletsedwa ndi kuchita zabwino, sipadzakhala mantha pa iwo ndiponso sadzadandaula.