(Allah) adati: “Nchiyani chakuletsa kumgwadira pamene ndakulamula?” (Satana) anati: “Ine ndine wabwino kuposa iye. Ine munandilenga ndi moto koma iye mudamulenga ndi dongo.”
Iye (chifukwa cha njiru yake yoopsa pa Adam) adati: “Tsono chifukwa chakuti mwandichita ine kukhala wopotoka, ndidzawakhalira (akapolo Anu ndi kuwabisalira) pa njira Yanu yoongoka (ndi cholinga chowasokeretsa).”
(Allah) adati: “Tuluka m’menemo, uli wonyozeka ndi wothamangitsidwa. Amene adzakutsata iwe mwa iwo, ndithudi, (ndikamponya ku Moto). Ndipo ndikaidzadzitsa Jahannam ndi inu nonse.”
(Kenako Allah adanena kwa Adam) “E iwe Adam! Khala ndi mkazi wako m’Munda wamtendere (sangalalani ndi zomwe zili m’menemo), idyani paliponse pamene mwafuna. Koma mtego uwu musawuyandikire kuopera kuti mungakhale m’gulu la odzichitira okha zoipa.”